Pular para o conteúdo
Publicidade

Provérbios 9

Za Nzeru ndi Uchitsiru

1 Nzeru inamanga nyumba yake;

inayimika nsanamira zake zisanu ndi ziwiri.

2 Inapha ziweto zake ndipo yasakaniza vinyo wake;

inasakaniza vinyo wake ndi kuyala tebulo lake.

3 Nzeruyo inatuma adzakazi ake,

kuti akakhale pamwamba penipeni pa mzinda ndi kukalengeza kuti,

4 "Aliyense amene ali munthu wamba, abwere kuno!"

Kwa onse opanda nzeru inkanena kuti,

5 "Bwerani, dzadyeni chakudya changa

ndipo dzamweni vinyo amene ndakonza.

6 Lekani zopusa zanu kuti mukhale ndi moyo;

yendani njira ya nzeru yomvetsa zinthu."

7 Aliyense amene amayesa kukonza munthu wonyoza amadziputira minyozo;

aliyense amene amadzudzula munthu woyipa amadetsa mbiri yake.

8 Usadzudzule munthu wonyoza kuti angadzadane nawe;

dzudzula munthu wanzeru ndipo adzakukonda.

9 Ukalangiza munthu wanzeru ndiye adzapitirira kukhala wanzeru;

ukaphunzitsa munthu wolungama ndiye adzawonjezera kuphunzira kwake.

10 Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru;

kudziwa Woyerayo ndiko kukhala womvetsa bwino zinthu.

11 Chifukwa cha ine nzeru, masiku ako adzachuluka,

ndipo zaka za moyo wako zidzawonjezeredwa.

12 Ngati ndiwe wanzeru, nzeru yakoyo idzakupindulitsa;

ngati ndiwe wonyoza ena, udzavutika wekha.

13 Uchitsiru ndi mkazi waphokoso,

wopulikira ndiponso wosadziwa zinthu.

14 Iye amakhala pa mpando, pa khomo la nyumba yake,

pamalo aatali a mu mzinda,

15 kuti aziyitana anthu ongodutsa,

amene akunka nayenda njira zawo.

16 Amati, "Onse amene ndi anthu wamba abwere kuno,"

ndipo kwa wopanda nzeru amati,

17 "Madzi akuba ndiye amatsekemera;

chakudya chodya mobisa ndi chokoma!"

18 Koma amunawo sadziwa kuti akufa ali kale komweko,

ndi kuti alendo ake alowa kale mʼmanda akuya.

Veja também