14 Kodi adzayitana bwanji amene sanamukhulupirire? Ndipo adzakhulupirira bwanji asanamve za Iye? Ndipo adzamva bwanji popanda wina kulalikira kwa iwo? 15 Ndipo iwo adzalalikira bwanji osatumidwa? Kwalembedwa kuti, "Akongoladi mapazi a iwo amene amabweretsa Uthenga Wabwino!"
16 Koma si onse amene anavomereza Uthenga Wabwino. Pakuti Yesaya akuti, "Ambuye, ndani amene wakhulupirira uthenga wathu?" 17 Motero, chikhulupiriro chimabwera pamene timva uthenga ndipo uthenga umamveka kuchokera ku mawu a Khristu.