17 Monga kwalembedwa kuti, "Ine ndakusandutsa kukhala kholo la mitundu yambiri." Iye ndiye kholo lathu pamaso pa Mulungu, amene anamukhulupirira, Mulungu amene amapereka moyo kwa akufa ndipo amapereka moyo kwa zinthu zopanda moyo.
18 Ngakhale zinali zosayembekezeka, Abrahamu anakhulupirira ndi chiyembekezo kuti adzakhala kholo la mitundu yambiri. Izi ndi monga zinanenedwa kwa iye kuti, "Ndi mmene adzakhalire ana ako ndi zidzukulu zako." 19 Iye sanafowoke mʼchikhulupiriro. Anadziwa choonadi cha thupi lake kuti linali lakufa popeza anali ndi zaka pafupifupi 100 ndiponso mimba ya Sara inali yowuma. 20 Komabe iye sanagwedezeke chifukwa chosakhulupirira pa zokhudzana ndi lonjezo la Mulungu. Iye analimbikitsidwa mʼchikhulupiriro chake ndi kupereka ulemerero kwa Mulungu. 21 Anatsimikiza mu mtima mwake kuti Mulungu anali ndi mphamvu yochita chomwe analonjeza.