Mtendere ndi Chimwemwe
1 Tsopano popeza tayesedwa olungama mwa chikhulupiriro, tili ndi mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. 2 Iyeyo ndiye amene anatsekulira njira mwachikhulupiriro yolowera mʼchisomo mʼmene takhazikikamo. Ndipo tikukondwerera chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu. 3 Koma si pokhapo ayi, koma ife tikukondweranso mʼmasautso athu chifukwa tikudziwa kuti masautso amatiphunzitsa kupirira. 4 Ndipo kupirira kumabweretsa makhalidwe, makhalidwe amabweretsa chiyembekezo.