Publicidade

Romanos 6

12 Nʼchifukwa chake, musalole tchimo lilamulire matupi anu amene anafa kuti mumvere zilakolako zonyansa. 13 Musapereke ziwalo zathupi lanu ku tchimo, ngati zipangizo zamakhalidwe oyipa. Mʼmalo mwake, mudzipereke kwa Mulungu, ngati amene achoka ku imfa kupita ku moyo. Ndipo mupereke ziwalo zathupi lanu ngati zipangizo zachilungamo. 14 Tchimo silidzakhalanso ndi mphamvu pa inu, chifukwa Malamulo sakulamulira moyo wanu koma chisomo.

Ife Ndife Akapolo a Mulungu

15 Nʼchiyani tsono? Kodi tidzichimwa chifukwa sitikulamulidwa ndi Malamulo koma chisomo? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! 16 Kodi inu simudziwa kuti pamene mudzipereka kwa wina wake, kumumvera ngati akapolo, ndinu akapolo a amene mumumvera? Ngati ndinu akapolo a tchimo mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo akumvera, mudzakhala olungama pamaso pake. 17 Koma ayamikidwe Mulungu pakuti ngakhale munali akapolo a tchimo, munamvera ndi mtima wonse chiphunzitso chimene munalandira. 18 Inu munamasulidwa ku tchimo ndipo tsopano mwasanduka akapolo achilungamo.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-