14 Atamva zimenezi analiranso kwambiri, ndipo Oripa anapsompsona apongozi ake nawatsanzika, koma Rute anakakamirabe.
15 Naomi anati "Taona, mʼbale wako wabwerera kwawo kwa anthu ake ndi kwa milungu yake. Bwerera nawenso umulondole mʼbale wako."
16 Koma Rute anayankha kuti, "Musandikakamize kuti ndikusiyeni kapena kuti ndibwerere osakutsatani. Kumene inu mupite ine ndipita komweko, ndipo kumene mukakhale inenso ndikakhala komweko. Abale anu adzakhala abale anga ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga. 17 Kumene mukafere inenso ndidzafera komweko ndipo komweko ndikayikidwa mʼmanda. Yehova andichite choyipa chingakule motani, ngati china chingatirekanitse ife kupatula imfa."