Pular para o conteúdo
Publicidade

RUTE 4

14 Ndipo amayi osiyanasiyana anati kwa Naomi. "Alemekezeke Yehova, amene lero lino sanakusiyeni nokha wopanda wachibale. Mwanayu dzina lake likhale lotchuka mu Israeli. 15 Mwanayo adzakupatseni moyo watsopano ndi kukuthandizani pa ukalamba wanu. Inde, mpongozi wanu amene amakukondani, amenenso waonetsa kuti ali wopambana kwa inu kuposa ana aamuna asanu ndi awiri, ndiye wakubalirani mwanayu."

16 Kenaka Naomi anatenga mwanayo namufukata ndipo anakhala mlezi.

17 Amayi achinansi ake anati, "Naomi ali ndi mwana wamwamuna." Ndipo anamutcha dzina lake Obedi. Iye anali abambo a Yese abambo ake a Davide.

Veja também

Rute
Ver todos os capítulos de Rute