Publicidade

Tiago 2

Chikhulupiriro ndi Ntchito Zabwino

14 Abale anga, phindu lake nʼchiyani ngati munthu anena kuti ali ndi chikhulupiriro koma chopanda ntchito zabwino? Kodi chikhulupiriro choterechi chingamupulumutse? 15 Tangoganizirani, mʼbale kapena mlongo amene ali ndi usiwa, ndipo alibe chakudya cha tsiku ndi tsiku. 16 Ngati mmodzi wa inu amuwuza kuti, "Pita ndi mtendere, ukafundidwe ndipo ukakhute," koma osamupatsa zimene akuzisowa, phindu lake nʼchiyani pamenepa? 17 Chomwechonso, chikhulupiriro chokha chopanda ntchito zabwino ndi chakufa.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-