Agradecimento a Deus
Agradecer a Deus é louvor, adoração e reconhecimento da sua soberania. Dai graças ao Senhor porque Ele é bom — a sua misericórdia dura para sempre!
Tiyeni tibwere pamaso pake ndi chiyamiko
ndipo mupembedzeni Iyeyo ndi zida zoyimbira ndi nyimbo.
Lowani ku zipata zake ndi chiyamiko
ndi ku mabwalo ake ndi matamando;
muyamikeni ndi kutamanda dzina lake.
Tamandani Yehova.
Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
pakuti chikondi chake ndi chosatha.
Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakuyamikani;
Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakukwezani.
Imbirani Yehova ndi mayamiko;
imbani nyimbo kwa Mulungu ndi pangwe.
Ine ndidzatamanda dzina la Mulungu mʼnyimbo,
ndidzalemekeza Iye ndi chiyamiko.
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa;
mtima wanga umadalira Iye, ndipo Ine ndathandizidwa.
Mtima wanga umalumphalumpha chifukwa cha chimwemwe
ndipo ndidzayamika Iye mʼnyimbo.
Tsopano Mulungu wathu, ife tikukuthokozani
ndi kutamanda dzina lanu laulemerero.
Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa china chilichonse, mwa pemphero ndi chidandaulo pamodzi ndi chiyamiko, perekani zopempha zanu kwa Mulungu.
Ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakumbukira inu.
Ndipo chilichonse chimene mungachite, kaya nʼkuyankhula, kaya nʼkugwira ntchito, muchite zonse mʼdzina la Ambuye Yesu, kuyamika kwa Mulungu Atate kudzera mwa Iye.
Ife timayamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu. Timakutchulani mʼmapemphero athu. Nthawi zonse timakumbukira ntchito yanu yachikhulupiriro, yachikondi ndi kupirira kwanu kwa chiyembekezo mwa Ambuye athu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu wathu ndi Atate.
Nthawi zonse ndimayamika Mulungu chifukwa cha inu chifukwa cha chisomo chake chopatsidwa kwa inu mwa Khristu Yesu.
Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Koma tithokoze Mulungu amene amatitsogolera nthawi zonse monga ogwidwa ku nkhondo a Khristu pa chipambano chake. Tsono amatigwiritsa ntchito yofalitsa ponseponse nzeru zodziwira Khristu ngati fungo labwino.
Tsono Mulungu amene amapereka mbewu kwa wofesa, ndiponso chakudya kuti adye, adzaperekanso mbewu mʼnkhokwe zanu ndi kuzichulukitsa. Iye adzachulukitsanso zipatso za chilungamo chanu. Adzakulemeretsani pa zonse kuti mukhale owolowamanja pa nthawi zonse. Ndipo kuwolowamanja kwanu kudzera mwa ife, kudzakhala kuthokoza kwa Mulungu.
Muziyankhulana wina ndi mnzake mawu a Masalimo, nyimbo za Mulungu ndi nyimbo za uzimu. Muziyimbira Ambuye movomerezana ndi mitima yanu. Muziyamika Mulungu Atate nthawi zonse chifukwa cha zonse, mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu.
Gonjeranani wina ndi mnzake, kuonetsa kuopa Khristu.
Atatenga malofu a buledi asanu ndi nsomba ziwiri, nayangʼana kumwamba, Iye anayamika nagawa malofu a bulediwo. Kenaka anawapatsa ophunzira ake kuti awapatse anthu. Ndipo anagawanso nsomba ziwirizo kwa onse. Onse anadya ndipo anakhuta, ndipo ophunzira ake anatola buledi ndi nsomba zotsalira zokwanira madengu khumi ndi awiri.