Publicidade

Jeremias 8

1 Yehova akuti, " ‘Pa nthawi imeneyo, mafupa a mafumu ndi a akuluakulu a ku Yuda, mafupa a ansembe ndi a aneneri, ndiponso mafupa a anthu a ku Yerusalemu adzafukulidwa. 2 Adzawamwaza pa nthaka kuyangʼana dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zonse zamlengalenga, zimene ankazikonda, kuzitumikira ndi kuzitsatira, kupemphako nzeru ndiponso kuzilambira. Mafupawo sadzawasonkhanitsa kapena kuwakwirira, koma adzakhala ngati ndowe pamwamba pa nthaka. 3 Otsala onse a mtundu woyipawu adzafuna imfa kopambana moyo kulikonse kumene ndidzawapirikitsirako, akutero Yehova Wamphamvuzonse.’ "

Tchimo ndi Chilango Chake

4 "Tsono awuze anthuwa, ‘Yehova akuti:

" ‘Kodi anthu akagwa sangadzukenso?

Munthu akasochera kodi sangathe kubwereranso?

5 Chifukwa chiyani nanga anthu awa akupitirirabe kuchimwa, osabwerera?

Chifukwa chiyani Yerusalemu akubwerera mʼmbuyo?

Iwo akangamira chinyengo;

akukana kubwerera.

6 Ine ndinatchera khutu kumvetsera

koma iwo sanayankhulepo zoona.

Palibe woyipa amene analapapo zoyipa zake,

nʼkumati, ‘Ine ndachita chiyani?’

Aliyense akutsatira njira yake

ngati kavalo wothamangira nkhondo.

7 Mbalame yotchedwa kakowa ija imadziwa

nthawi yake mlengalenga.

Koma nkhunda, namzeze ndi chingalu

zimadziwa nthawi yonyamukira ulendo,

koma anthu anga sadziwa

malamulo a Yehova.

8 " ‘Inu mukunena bwanji kuti,

‘Ndife anzeru ndipo timasunga malamulo a Yehova?’

Koma ndi alembi anu

amene akulemba zabodza.

9 Anthu anzeru achita manyazi;

athedwa nzeru ndipo agwidwa.

Iwo anakana mawu a Yehova.

Nanga tsono nzeru zawo ziwapinduliranji?

10 Nʼchifukwa chake akazi awo ndidzawapereka kwa amuna ena

ndipo minda yawo ndidzayipereka kwa amene adzawagonjetse.

Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,

onse ali ndi khalidwe lofuna kupeza chuma mwakuba.

Aneneri pamodzi ndi ansembe omwe,

onse amachita zachinyengo.

11 Iwo amapoletsa zilonda za anthu anga

pamwamba chabe

nʼkumati, ‘Mtendere, mtendere,’

pamene palibe mtendere.

12 Kodi amachita manyazi akamachita zonyansazi?

Ayi, alibe manyazi ndi pangʼono pomwe;

iwo sadziwa nʼkugwetsa nkhope komwe.

Choncho iwo adzagwera pakati pa anzawo amene agwa kale;

adzagwa pansi tsiku limene ndidzawalanga,

akutero Yehova.

13 " ‘Ndidzatenga zokolola zawo,

Sipadzakhalanso mphesa pa mpesa

kapena nkhuyu pa mkuyu,

ndipo masamba ake adzawuma.

Zinthu zimene ndinawapatsa

ndidzawachotsera.’ "

14 Koma amati, "Tikukhala pano chifukwa chiyani?

Tiyeni tonse pamodzi

tithawire ku mizinda yotetezedwa

ndi kukafera kumeneko.

Pakuti Yehova Mulungu wathu watsimikiza kuti tiyenera kufa.

Watipatsa madzi aululu kuti timwe,

chifukwa tamuchimwira.

15 Tinkayembekezera mtendere

koma palibe chabwino chomwe chinachitika,

tinkayembekezera kuchira

koma tinakumana ndi zoopsa zokhazokha.

16 Kulira kwa ngʼombe zazimuna za mdani

kukumveka kuchokera ku Dani;

dziko lonse likunjenjemera

chifukwa cha kulira kwa akavalowo.

Akubwera kudzawononga dziko

ndi zonse zimene zili mʼmenemo.

Adzawononga mzinda ndi onse okhalamo."

17 Yehova akuti, "Onani, ndikukutumizirani njoka zaululu,

mphiri zimene munthu sangathe kuzilodza,

ndipo zidzakulumani,"

18 Ndadzazidwa ndi chisoni kwambiri,

mtima wanga walefukiratu.

19 Imvani kulira kwa anthu anga

kuchokera ku dziko lakutali:

akuti, "Kodi Yehova sali ku Ziyoni?

Kodi mfumu yake sili kumeneko?"

"Chifukwa chiyani akundiputa ndi mafano awo osema,

ndi milungu yawo yachilendo?"

20 "Nthawi yokolola yapita,

chilimwe chapita,

koma sitinapulumuke."

21 Chifukwa cha mavuto a anthu anga, ine ndikumva kuwawa;

ndikungolira ndipo mantha aakulu andigwira.

22 Kodi ku Giliyadi kulibe mankhwala ochiritsa?

Kodi kumeneko kulibe singʼanga?

Nanga chifukwa chiyani mabala

a anthu anga sanapole?

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-16_18-40-07-