Publicidade

Jeremias 47

Uthenga Wonena za Afilisti

1 Uthenga umene Yehova anamupatsa mneneri Yeremiya wonena za Afilisti, Farao asanathire nkhondo Gaza ndi uwu:

2 Yehova akuti,

"Taonani mmene madzi akubwerera kuchokera kumpoto;

adzasanduka mtsinje wosefukira ndi a mkokomo.

Adzasefukira mʼdziko monse ndi kumiza chilichonse mʼmenemo,

mizinda ndi onse okhala mʼmenemo.

Anthu adzafuwula;

anthu onse okhala mʼdzikomo adzalira

3 akadzamva mgugu wa ngʼombe zazimuna zothamanga,

phokoso la magaleta ake

ndi kulira kwa mikombero yake.

Makolo sadzatembenuka kuti athandize ana awo;

manja awo adzangoti khoba.

4 Pakuti tsiku lafika

lowononga Afilisti onse

ndi kupha onse otsala,

onse amene akanatha kuthandiza Turo ndi Sidoni.

Yehova ali pafupi kuwononga Afilisti,

otsala ochokera ku zilumba za ku Kafitori.

5 Anthu a ku Gaza ameta mipala;

anthu a ku Asikeloni akhala chete.

Inu otsala a ku chigwa,

mudzakhala mukudzichekacheka mpaka liti?

6 "Mukulira kuti, ‘Aa, lupanga la Yehova,

kodi udzapumula liti?

Bwerera mʼmalo ako;

ukhale momwemo ndipo ukhale chete.’

7 Koma lupangalo lidzapumula bwanji

pamene Yehova walilamulira

kuti lithire nkhondo

Asikeloni ndi anthu a mʼmbali mwa nyanja?"

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_14-04-22-