Publicidade

Ajuda ao próximo

Por Bíblia Online

Ajudar o próximo é mandamento de Deus e expressão prática da fé. A Bíblia ensina que a fé sem obras é morta — e que servir ao menor dos irmãos é servir a Cristo.

Pakuti ndinali ndi njala ndipo munandipatsa chakudya, ndinali ndi ludzu ndipo munandipatsa madzi akumwa, ndinali mlendo ndipo munandilandira, ndinali wausiwa ndipo munandiveka, ndinali wodwala ndipo munandisamalira, ndinali ku ndende ndipo inu munandiyendera.

"Ndipo olungamawo adzamuyankha kuti, Ambuye ndi liti tinakuonani muli ndi njala ndipo tinakudyetsani, kapena ludzu ndipo tinakupatsani madzi akumwa? Ndi liti tinakuonani muli mlendo ndipo tinakulandirani, kapena wa usiwa ndipo tinakuvekani? Ndi liti tinakuonani mutadwala kapena ku ndende ndipo tinakuyenderani?

"Mfumu idzayankha kuti, Zoonadi, ndikuwuzani kuti chilichonse chimene munachitira mmodzi wa abale anga onyozekawa munandichitira Ine.

Wina akakupempha kanthu umupatse, ndipo wofuna kubwereka usamukanize.

Momwemonso kuwunika kwanu kuwale pamaso pa anthu kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kulemekeza Atate anu akumwamba.

Perekani ndipo mudzapatsidwa. Adzakupatsani mʼthumba mwanu muyeso wabwino, wotsenderezeka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Pakuti muyeso umene mumagwiritsa ntchito, ndi omwewo adzakuyeserani."

Gulu la anthuwo linafunsa kuti, "Nanga tsono tichite chiyani?"

Yohane anayankha kuti, "Munthu amene ali ndi malaya awiri apatseko amene alibe, ndi amene ali ndi chakudya achitenso chimodzimodzi."

Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupereke kwa osauka. Dzipezereni zikwama zandalama zimene sizidzatha, ndi kudzikundikira chuma chomwe sichidzatha kumwamba, kumene mbala sizingafikeko, ndipo dzimbiri silingawononge. Popeza kumene kuli chuma chanu, mtima wanunso udzakhala komweko."

Lamulo langa ndi ili: Kondanani wina ndi mnzake monga Ine ndakonda inu.

Palibe munthu ali ndi chikondi choposa ichi, choti munthu nʼkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.

Pa zonse zimene ndinachita, ndinakuonetsani kuti pogwira ntchito molimbika motere tiyenera kuthandiza ofowoka, pokumbukira mawu a Ambuye Yesu akuti, Kupereka kumadalitsa kuposa kulandira.’ "

Atanena zimenezi, anagwada pansi pamodzi ndi ena onse, napemphera. Onse analira pamene amamukumbatira ndi kupsompsona. Chimene chinamvetsa chisoni kwambiri ndi mawu ake akuti sadzaonanso nkhope yake. Kenaka iwo anamuperekeza ku sitima yapamadzi.

Gawanani ndi anthu a Mulungu amene ali ndi chosowa. Cherezani alendo.

Ife amene tili ndi chikhulupiriro champhamvu tiziwalezera mtima anthu ofowoka, ndipo tisamadzikondweretse tokha.

Thandizanani kusenza zolemetsa zanu, ndipo mʼnjira imeneyi mudzakwanitsa lamulo la Khristu.

Iye amene wakhala akuba asabenso, koma agwire ntchito ndi kuchita kenakake kaphindu ndi manja ake, kuti akhale ndi kenakake kogawana ndi amene akusowa.

Musamangofuna zokomera inu nokha koma aliyense azifuna zokomeranso ena.

Chikhulupiriro ndi Ntchito Zabwino

Abale anga, phindu lake nʼchiyani ngati munthu anena kuti ali ndi chikhulupiriro koma chopanda ntchito zabwino? Kodi chikhulupiriro choterechi chingamupulumutse? Tangoganizirani, mʼbale kapena mlongo amene ali ndi usiwa, ndipo alibe chakudya cha tsiku ndi tsiku. Ngati mmodzi wa inu amuwuza kuti, "Pita ndi mtendere, ukafundidwe ndipo ukakhute," koma osamupatsa zimene akuzisowa, phindu lake nʼchiyani pamenepa? Chomwechonso, chikhulupiriro chokha chopanda ntchito zabwino ndi chakufa.

Ngati wina ali ndi chuma ndipo nʼkuona mʼbale wake akusowa, koma wosamvera chisoni, kodi mwa iyeyo muli chikondi cha Mulungu?

Amene amakomera mtima osauka amachita ngati wakongoletsa Yehova,

ndipo Yehovayo ndiye adzamubwezere.

Anthu osauka sadzatha mʼdziko lanu. Chomwecho ndikukulamulani kuti mukhale ofewa manja kwa abale anu ndi kwa osauka, osowa mʼdziko mwanu.

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-