Publicidade

Salmos 137

1 Mʼmbali mwa mitsinje ya ku Babuloni tinakhala pansi ndi kulira

pamene tinakumbukira Ziyoni.

2 Kumeneko, pa mitengo ya misondozi

tinapachika apangwe athu,

3 pakuti anthu otigwira ukapolo anatipempha kuti tiyimbe nyimbo.

Otizunza athu anafuna nyimbo zachisangalalo;

iwo anati, "Tiyimbireni imodzi mwa nyimbo za ku Ziyoni!"

4 Tingayimbe bwanji nyimbo za Yehova

mʼdziko lachilendo?

5 Ndikakuyiwala iwe Yerusalemu,

dzanja langa lamanja liyiwale luso lake.

6 Lilime langa limamatire ku nkhama za mʼkamwa mwanga

ndikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu,

ngati sindiyesa iwe

chimwemwe changa chachikulu.

7 Kumbukirani, Inu Yehova, zimene Aedomu anachita

pa tsiku limene Yerusalemu anagonja.

Iwowo anafuwula kuti, "Mugwetseni pansi, mugwetseni pansi

mpaka pa maziko ake!"

8 Iwe mwana wa mkazi wa Babuloni, woyenera kuwonongedwa,

wodalitsika ndi yemwe adzakubwezera

pa zimene watichitira.

9 Amene adzagwira makanda ako

ndi kuwakankhanthitsa pa miyala.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-15_21-32-39-