Publicidade

Salmos 95

1 Bwerani, tiyeni timuyimbire Yehova mwachimwemwe,

tiyeni tifuwule kwa Thanthwe la chipulumutso chathu

2 Tiyeni tibwere pamaso pake ndi chiyamiko

ndipo mupembedzeni Iyeyo ndi zida zoyimbira ndi nyimbo.

3 Pakuti Yehova ndi Mulungu wamkulu,

mfumu yayikulu pamwamba pa milungu yonse.

4 Mʼmanja mwake muli maziko ozama a dziko lapansi,

ndipo msonga za mapiri ndi zake.

5 Nyanja ndi yake, pakuti anayilenga ndi Iye,

ndipo manja ake anawumba mtunda wowuma.

6 Bwerani, tiyeni tiwerame pomulambira,

tiyeni tigwade pamaso pa Yehova Mlengi wathu;

7 pakuti Iye ndiye Mulungu wathu

ndipo ife ndife anthu a pabusa pake,

ndi nkhosa za mʼdzanja lake.

Lero ngati inu mumva mawu ake,

8 musawumitse mitima yanu monga momwe munachitira pa Meriba,

monga munachitira tsiku lija pa Masa mʼchipululu.

9 Kumene makolo anu anandiyesa ndi kundiputa,

ngakhale anaona zimene Ine ndinazichita.

10 Kwa zaka makumi anayi ndinali wokwiya ndi mʼbado umenewo;

ndipo ndinati, "Iwo ndi anthu amene mitima yawo imasochera

ndipo sanadziwe njira zanga."

11 Choncho ndili chikwiyire, ndinalumbira kuti,

"Iwowa sadzalowa ku malo anga a mpumulo."

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-15_21-32-39-