Publicidade

Salmos 75

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe, potsata mayimbidwe a "Musawononge." Salimo la Asafu. Nyimbo.

1 Tikuthokoza Inu Mulungu,

tikuthokoza, pakuti dzina lanu lili pafupi nafe,

anthutu amafotokoza za ntchito zanu zodabwitsa.

2 Mumati, "Ine ndimayika nthawi yoyenera,

ndine amene ndimaweruza mwachilungamo.

3 Pamene dziko lapansi ndi anthu ake onse anjenjemera,

ndine amene ndimagwiriziza mizati yake molimba.

Sela

4 Kwa odzitama ndikuti, ‘Musadzitamenso,’

ndipo kwa oyipa, ‘Musatukulenso nyanga zanu.

5 Musatukule nyanga zanu motsutsana ndi kumwamba;

musayankhule ndi khosi losololoka.’ "

6 Kugamula milandu sikuchokera kummawa kapena kumadzulo

kapena ku chipululu.

7 Koma ndi Mulungu amene amaweruza:

Iyeyo amatsitsa wina, nakwezanso wina.

8 Mʼdzanja la Yehova muli chikho

chodzaza ndi vinyo wochita thovu, wosakanizidwa ndi zokometsera;

Iye amamutsanulira pansi ndipo onse oyipa a dziko lapansi

amamwa ndi senga zake zonse.

9 Kunena za ine, ndidzalengeza izi kwamuyaya;

ndidzayimba matamando kwa Mulungu wa Yakobo.

10 Ndidzadula nyanga za onse oyipa

koma nyanga za olungama zidzakwezedwa.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-15_21-32-39-