Publicidade

Salmos 57

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a "Musawononge." Ndakatulo ya Davide, pamene anathawa Sauli kupita ku phanga.

1 Mundichitire chifundo, Inu Mulungu mundichitire chifundo,

pakuti mwa Inu moyo wanga umathawiramo.

Ndidzathawira mu mthunzi wa mapiko anu

mpaka chiwonongeko chitapita.

2 Ine ndikufuwulira kwa Mulungu Wammwambamwamba,

kwa Mulungu amene amakwaniritsa cholinga chake pa ine.

3 Mulungu amanditumizira kuchokera kumwamba ndi kundipulumutsa,

kudzudzula iwo amene akundithamangitsa kwambiri.

Mulungu amatumiza chikondi chake ndi kukhulupirika kwake.

4 Ine ndili pakati pa mikango,

ndagona pakati pa zirombo zolusa;

anthu amene mano awo ndi milomo yawo ndi mivi,

malilime awo ndi malupanga akuthwa.

5 Mukwezekedwe Inu Mulungu, kuposa mayiko onse akumwamba;

mulole kuti ulemerero wanu ukhale pa dziko lonse lapansi.

6 Iwo anatchera mapazi anga ukonde

ndipo ndinawerama pansi mosautsidwa.

Anakumba dzenje mʼnjira yanga

koma agweramo okha mʼmenemo.

7 Mtima wanga ndi wokhazikika, Inu Mulungu

mtima wanga ndi wokhazikika.

Ndidzayimba nyimbo, nyimbo yake yamatamando.

8 Dzuka moyo wanga!

Dzukani zeze ndi pangwe!

Ndidzadzuka mʼbandakucha.

9 Ndidzakutamandani Ambuye, pakati pa mitundu ya anthu,

ndidzayimba za Inu pakati pa mayiko.

10 Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu, kufikira ku mayiko akumwamba;

kukhulupirika kwanu kwafika ku mitambo.

11 Mukwezekedwe Inu Mulungu kuposa mayiko akumwamba,

mulole kuti ulemerero wanu ukhale pa dziko lonse lapansi.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-15_21-32-39-