Publicidade

Salmos 39

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Kwa Yedutuni. Salimo la Davide.

1 Ndinati, "Ndidzasamalira njira zanga

ndipo ndidzasunga lilime langa kuti ndisachimwe;

ndidzatseka pakamwa panga ndi chitsekerero

nthawi yonse imene woyipa ali pamaso panga."

2 Koma pamene ndinali chete

osanena ngakhale kanthu kalikonse kabwino

mavuto anga anachulukirabe.

3 Mtima wanga unatentha mʼkati mwanga,

ndipo pamene ndinkalingalira, moto unayaka;

kenaka ndinayankhula ndi lilime langa:

4 "Yehova ndionetseni mathero a moyo wanga

ndi chiwerengero cha masiku anga;

mundidziwitse kuti moyo wanga ndi wosakhalitsa motani.

5 Inu mwachititsa kuti masiku anga akhale ochepa kwambiri,

kutalika kwa zaka zanga ndi kopanda phindu pamaso panu;

moyo wa munthu aliyense ndi waufupi.

Sela

6 Munthu ali ngati chithunzithunzi chake pamene akuyenda uku ndi uku:

Iye amangovutika koma popanda phindu;

amadzikundikira chuma, osadziwa kuti chidzakhala chayani.

7 "Koma tsopano Ambuye kodi ndifunanso chiyani?

Chiyembekezo changa chili mwa Inu.

8 Pulumutseni ku zolakwa zanga zonse;

musandisandutse chonyozeka kwa opusa.

9 Ine ndinali chete; sindinatsekule pakamwa panga

pakuti Inu ndinu amene mwachita zimenezi.

10 Chotsani mkwapulo wanu pa ine;

ndagonjetsedwa ndi nkhonya ya dzanja lanu.

11 Inu mumadzudzula ndi kulanga anthu chifukwa cha tchimo lawo;

mumawononga chuma chawo monga njenjete;

munthu aliyense ali ngati mpweya.

Sela

12 "Imvani pemphero langa Inu Yehova,

mverani kulira kwanga kopempha thandizo;

musakhale chete pamene ndikulirira kwa Inu,

popeza ndine mlendo wanu wosakhalitsa;

monga anachitira makolo anga onse.

13 Musandiyangʼane mwaukali, choncho ndidzatha kusangalala

ndisanafe ndi kuyiwalika."

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-16_06-50-08-