Publicidade

Salmos 2

1 Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu?

Akonzekeranji zopanda pake anthu?

2 Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo;

ndipo olamulira asonkhana pamodzi

kulimbana ndi Ambuye

ndi wodzozedwa wakeyo.

3 Iwo akunena kuti, "Tiyeni timasule magoli awo

ndipo titaye zingwe zawo."

4 Wokhala mmwamba akuseka;

Ambuye akuwanyoza iwowo.

5 Ndipo iye awadzudzula mu mkwiyo wake

ndi kuwaopseza mu ukali wake, kunena kuti,

6 "Ine ndakhazikitsa mfumu yanga

pa Ziyoni, phiri langa loyera."

7 Ine ndidzalengeza zimene Yehova walamula:

Iye anati kwa Ine, "Iwe ndiwe mwana wanga;

lero Ine ndakhala Atate ako.

8 Tandipempha,

ndipo ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu ikhale cholowa chako;

malekezero a dziko lapansi kuti akhale chuma chako.

9 Iweyo udzawalamulira ndi ndodo yaufumu yachitsulo;

udzawaphwanya zidutswazidutswa ngati zowumba zadothi."

10 Kotero, inu mafumu, chenjerani;

chenjezedwani, inu olamulira a dziko lapansi.

11 Tumikirani Yehova mwa mantha

ndi kukondwerera ulamuliro wake monjenjemera.

12 Mpsopsoneni mwanayo kuti angakwiye;

kuti mungawonongedwe mʼnjira zanu,

pakuti ukali wake utha kuuka mʼkanthawi kochepa.

Odala ndi onse amene amathawira kwa Iye.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-16_06-50-08-