Publicidade

Salmos 42

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora.

1 Monga mbawala ipuma wefuwefu kufunafuna mitsinje yamadzi,

kotero moyo wanga upuma wefuwefu kufunafuna Inu Mulungu.

2 Moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Mulungu, lofuna Mulungu wamoyo.

Kodi ndipite liti kukakumana ndi Mulungu?

3 Misozi yanga yakhala chakudya changa

usana ndi usiku,

pamene anthu akunena kwa ine tsiku lonse kuti,

"Mulungu wako ali kuti?"

4 Zinthu izi ndimazikumbukira

pamene ndikukhuthula moyo wanga:

momwe ndinkapitira ndi gulu lalikulu,

kutsogolera mayendedwe a ku Nyumba ya Mulungu

ndi mfuwu yachimwemwe ndi mayamiko

pakati pa anthu a pa chikondwerero.

5 Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni, iwe moyo wanga?

Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga?

Yembekezera Mulungu,

pakuti ndidzamulambirabe,

Mpulumutsi wanga ndi 6 Mulungu wanga.

Moyo wanga uli ndi chisoni mʼkati mwanga

kotero ndidzakumbukira Inu

kuchokera ku dziko la Yorodani,

ku mitunda ya Herimoni kuchokera ku phiri la Mizara.

7 Madzi akuya akuyitana madzi akuya

mu mkokomo wa mathithi anu;

mafunde anu onse obwera mwamphamvu

andimiza.

8 Koma usana Yehova amalamulira chikondi chake,

nthawi ya usiku nyimbo yake ili nane;

pemphero kwa Mulungu wa moyo wanga.

9 Ine ndikuti kwa Mulungu Thanthwe langa,

"Nʼchifukwa chiyani mwandiyiwala?

Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira,

woponderezedwa ndi mdani?"

10 Mafupa anga ali ndi ululu wakufa nawo

pamene adani anga akundinyoza,

tsiku lonse akunena kuti,

"Mulungu wako ali kuti?"

11 Bwanji ukumva chisoni,

iwe mtima wanga?

Chifukwa chiyani ukuvutika chonchi mʼkati mwanga?

Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamutamandanso,

Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-16_18-40-07-