Pular para o conteúdo
Publicidade

MASALIMO 82

Salimo la Asafu.

1 Mulungu akutsogolera msonkhano waukulu;

Iye akuweruza pakati pa "milungu."

2 "Mudzateteza osalungama mpaka liti,

ndi kukondera anthu oyipa?

3 Tetezani anthu ofowoka ndi amasiye;

mukhazikitse ufulu wa anthu osauka ndi ozunzika.

4 Landitsani anthu ofowoka ndi osowa;

apulumutseni mʼdzanja la anthu oyipa.

5 "Iwo sadziwa kanthu, sazindikira kalikonse.

Amayendayenda mu mdima;

maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.

6 "Ndinati, Inu ndinu Mulungu,

nonsenu ndinu ana a Wammwambamwamba.

7 Koma mudzafa ngati anthu wamba;

mudzagwa ngati wolamula wina aliyense."

8 Dzukani Inu Mulungu, weruzani dziko lapansi,

pakuti mayiko onse ndi cholowa chanu.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também