Publicidade

Salmos 58

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a "Musawononge." Ndakatulo ya Davide.

1 Kodi inu olamulira mumayankhuladi molungama?

Kodi mumaweruza mwachilungamo pakati pa anthu?

2 Ayi, mʼmitima mwanu mumakonzekera zosalungama,

ndipo manja anu amatulutsa zachiwawa pa dziko lapansi.

3 Ngakhale kuchokera tsiku lawo lobadwa oyipa amasochera;

kuchokera mʼmimba ya amayi awo, iwo ndi otayika ndipo amayankhula mabodza.

4 Ululu wawo uli ngati ululu wa njoka,

ngati uja wa mphiri imene yatseka mʼmakutu mwake.

5 Imene simva liwu la munthu wamatsenga,

ngakhale akhale wa luso lotani munthu wamatsengayo.

6 Gululani mano mʼkamwa mwawo, Inu Mulungu,

Yehova khadzulani mano a mikango!

7 Mulole kuti asowe ngati madzi oyenda

pamene iwo akoka uta mulole kuti mivi yawo ikhale yosathwa.

8 Akhale ngati nkhono imene imasungunuka pamene ikuyenda;

ngati mwana wakufa asanabadwe, iwo asaone dzuwa.

9 Miphika yanu isanagwire moto waminga ya mkandankhuku,

kaya iyo ndi yobiriwira kapena yowuma, oyipa adzachotsedwa.

10 Olungama adzasangalala poona kubwezera chilango,

pamene adzasambitsa mapazi awo mʼmagazi a anthu oyipa.

11 Ndipo anthu adzanena kuti,

"Zoonadi, olungama amalandirabe mphotho;

zoonadi kuli Mulungu amene amaweruza dziko lapansi."

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-16_18-40-07-