Publicidade

Salmos 110

Salimo la Davide.

1 Yehova akuwuza Mbuye wanga kuti,

"Khala ku dzanja langa lamanja

mpaka nditasandutsa adani ako

kukhala chopondapo mapazi ako."

2 Yehova adzakuza ndodo yamphamvu ya ufumu wako kuchokera mʼZiyoni;

udzalamulira pakati pa adani ako.

3 Ankhondo ako adzakhala odzipereka

pa tsiku lako la nkhondo.

Atavala chiyero chaulemerero,

kuchokera mʼmimba ya mʼbandakucha,

udzalandira mame a unyamata wako.

4 Yehova walumbira

ndipo sadzasintha maganizo ake:

"Ndiwe wansembe mpaka muyaya

monga mwa unsembe wa Melikizedeki."

5 Ambuye ali kudzanja lako lamanja;

Iye adzaponda mafumu pa tsiku la ukali wake.

6 Adzaweruza anthu a mitundu ina,

adzadzaza dziko lapansi ndi mitembo ndipo adzaphwanya olamulira a pa dziko lonse lapansi.

7 Iye adzamwa mu mtsinje wa mʼmbali mwa njira;

choncho adzaweramutsa mutu wake.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-15_21-32-39-