Publicidade

Salmos 52

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe, ndakatulo ya Davide; pamene Doegi Mwedomu anapita kwa Sauli ndi kunena kuti "Davide wapita ku nyumba ya Ahimeleki."

1 Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira ndi zoyipa, iwe munthu wamphamvu?

Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira tsiku lonse,

iwe munthu wochititsa manyazi pamaso pa Mulungu?

2 Tsiku lonse umakhalira kuganizira za kuwononga ena;

lilime lako lili ngati lumo lakuthwa,

ntchito yako nʼkunyenga.

3 Iwe umakonda choyipa mʼmalo mwa kuyankhula choonadi.

Umakonda kunama kupambana kuyankhula zoona.

Sela

4 Umakonda mawu onse opweteka,

iwe lilime lachinyengo!

5 Zoonadi Mulungu adzakutsitsa kupita ku chiwonongeko chamuyaya:

iye adzakukwatula ndi kukuchotsa mʼtenti yako;

iye adzakuzula kuchoka mʼdziko la amoyo.

6 Olungama adzaona zimenezi ndi kuchita mantha;

adzamuseka nʼkumanena kuti,

7 "Pano tsopano pali munthu

amene sanayese Mulungu linga lake,

koma anakhulupirira chuma chake chambiri

nalimbika kuchita zoyipa!"

8 Koma ine ndili ngati mtengo wa olivi

wobiriwira bwino mʼnyumba ya Mulungu;

ndimadalira chikondi chosatha cha Mulungu

kwa nthawi za nthawi.

9 Ine ndidzakutamandani kwamuyaya chifukwa cha zimene mwachita;

chifukwa cha zimene mwachita; mʼdzina lanu ndidzayembekezera

pakuti dzina lanulo ndi labwino. Ndidzakutamandani pamaso pa oyera mtima anu.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-15_21-32-39-