Publicidade

Salmos 54

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Ndakatulo ya Davide. Pamene anthu a ku Zifi anapita kwa Sauli ndipo anati, "Kodi Davide sakubisala pakati pathu."

1 Pulumutseni Inu Mulungu, mwa dzina lanu;

onetsani kuti ndine wosalakwa mwamphamvu yanu.

2 Imvani pemphero langa, Inu Mulungu

mvetserani mawu a pakamwa panga.

3 Alendo akundithira nkhondo;

anthu ankhanza akufunafuna moyo wanga,

anthu amene salabadira za Mulungu.

4 Zoonadi Mulungu ndi thandizo langa;

Ambuye ndiye amene amandichirikiza ine.

5 Lolani kuti choyipa chifike pa iwo amene amandichita chipongwe;

mwa kukhulupirika kwanu awonongeni.

6 Ine ndidzapereka nsembe yaufulu kwa Inu;

ndidzatamanda dzina lanu, Inu Yehova,

pakuti ndi labwino.

7 Pakuti Iyeyo wandipulumutsa ku masautso anga onse,

ndipo maso anga apenya kupambana kwa pa adani anga.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-15_21-32-39-