Publicidade

Salmos 140

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

1 Landitseni Yehova kwa anthu oyipa;

tetezeni kwa anthu ankhanza,

2 amene mu mtima mwawo amakonza zinthu zoyipa

ndi kuyambitsa nkhondo tsiku lililonse.

3 Iwo amanola malilime awo kukhala akuthwa ngati a njoka;

pa milomo yawo pali ululu wa mamba.

Sela

4 Tetezeni Inu Yehova, kwa anthu oyipa;

tchinjirizeni kwa anthu ankhanza

amene amakonza zokola mapazi anga.

5 Anthu odzikuza anditchera msampha mobisika;

iwo atchera zingwe za maukonde awo

ndipo anditchera misampha pa njira yanga.

Sela

6 Inu Yehova, ine ndikuti, "Ndinu Mulungu wanga."

Imvani kupempha kwanga Yehova.

7 Inu Ambuye Wamphamvuzonse, Mpulumutsi wanga wamphamvu,

mumateteza mutu wanga tsiku lankhondo.

8 Musawapatse anthu oyipa zokhumba zawo, Inu Yehova;

musalole kuti zokonza zawo zitheke,

mwina iwo adzayamba kunyada.

Sela

9 Mitu ya amene andizungulira

iphimbidwe ndi masautso amene milomo yawo yayambitsa.

10 Makala amoto agwere pa iwo;

aponyedwe pa moto,

mʼmaenje amatope, asatulukemonso.

11 Musalole kuti anthu achipongwe akhazikike mʼdziko;

choyipa chilondole anthu ankhanza.

12 Ndikudziwa kuti Yehova amapereka chiweruzo cholungama kwa anthu osauka,

ndipo amateteza zolinga za anthu osowa.

13 Zoonadi anthu olungama adzatamanda dzina lanu,

ndipo anthu owongoka mtima adzakhala pamaso panu.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-15_21-32-39-