Publicidade

Salmos 46

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora. Nyimbo ya anamwali.

1 Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu,

thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto.

2 Nʼchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisunthike,

ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja,

3 ngakhale madzi ake atakokoma ndi kuchita thovu,

ngakhale mapiri agwedezeke ndi kukokoma kwake.

4 Kuli mtsinje umene njira zake za madzi zimasangalatsa mzinda wa Mulungu,

malo oyera kumene Wammwambamwamba amakhalako.

5 Mulungu ali mʼkati mwake, iwo sudzagwa;

Mulungu adzawuthandiza mmawa.

6 Mitundu ikupokosera, mafumu akugwa;

Iye wakweza mawu ake, dziko lapansi likusungunuka.

7 Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife,

Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.

8 Bwerani kuti mudzaone ntchito za Yehova,

chiwonongeko chimene wachibweretsa pa dziko lapansi.

9 Iye amathetsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi;

Iye amathyola uta ndi kupindapinda mkondo;

amatentha zishango ndi moto.

10 Iye akuti, "Khala chete, ndipo dziwa kuti ndine Mulungu;

ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu;

ine ndidzakwezedwa mʼdziko lapansi."

11 Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife,

Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-15_21-32-39-