Pular para o conteúdo
Publicidade

MASALIMO 11

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

1 Mwa Yehova ine ndimathawiramo.

Nanga mungathe bwanji kunena kwa ine kuti,

"Thawira ku phiri lako ngati mbalame.

2 Pakuti taona oyipa akunga mauta awo;

ayika bwino mivi yawo pa zingwe za uta,

pobisala pawo kuti alase

olungama mtima.

3 Tsono ngati maziko awonongeka,

olungama angachite chiyani?"

4 Yehova ali mʼNyumba yake yoyera;

Yehova ali pa mpando wake waufumu kumwamba.

Iye amayangʼanitsitsa ana a anthu;

maso ake amawayesa.

5 Yehova amayesa olungama,

koma moyo wake umadana ndi oyipa,

amene amakonda zachiwawa.

6 Iye adzakhuthulira pa oyipa

makala amoto ndi sulufule woyaka;

mphepo yotentha idzakhala yowayenera.

7 Pakuti Yehova ndi wolungama,

Iye amakonda chilungamo;

ndipo anthu olungama adzaona nkhope yake.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também