Pular para o conteúdo
Publicidade

MASALIMO 129

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1 "Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,"

anene tsono Israeli;

2 "Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,

koma sanandipambane.

3 Anthu otipula analima pa msana panga

ndipo anapangapo mizere yayitali:

4 Koma Yehova ndi wolungama;

Iye wandimasula ku zingwe za anthu oyipa."

5 Onse amene amadana ndi Ziyoni

abwezedwe pambuyo mwamanyazi.

6 Akhale ngati udzu womera pa denga la nyumba,

umene umafota usanakule;

7 sungadzaze manja a owumweta

kapena manja a omanga mitolo.

8 Odutsa pafupi asanene kuti,

"Dalitso la Yehova lili pa inu;

tikukudalitsani mʼdzina la Yehova."

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também