Publicidade

Salmos 122

Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1 Ndinakondwera atandiwuza kuti,

"Tiyeni ku nyumba ya Yehova."

2 Mapazi athu akuyima mʼzipata

zako, Iwe Yerusalemu.

3 Yerusalemu anamangidwa ngati mzinda

umene uli wothithikana pamodzi.

4 Kumeneko ndiye kumene kumapita mafuko,

mafuko a Yehova,

umboni wa kwa Israeli,

kuti atamande dzina la Yehova.

5 Kumeneko anayikako mipando yaufumu yachiweruzo,

mipando yaufumu ya nyumba ya Davide.

6 Pemphererani mtendere wa Yerusalemu:

"Iwo amene amakukonda iwe zinthu ziwayendere bwino.

7 Mukhale mtendere mʼkati mwa makoma ako,

ndipo mʼnyumba zako zaufumu mukhale chitetezo."

8 Chifukwa cha abale anga ndi abwenzi anga

ndidzati, "Mtendere ukhale mʼkati mwako."

9 Chifukwa cha Nyumba ya Yehova Mulungu wathu,

ndidzakufunira zabwino.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-15_21-32-39-