Publicidade

Salmos 70

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pempho.

1 Fulumirani Mulungu kundipulumutsa;

Yehova bwerani msanga kudzandithandiza.

2 Iwo amene akufunafuna moyo wanga

achititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa;

onse amene akukhumba chiwonongeko changa

abwezedwe mopanda ulemu.

3 Onse amene akunena kwa ine kuti, "Aha, aha,"

abwerere chifukwa cha manyazi awo.

4 Koma onse amene akufunafuna Inu

akondwere ndi kusangalala mwa Inu;

iwo amene amakonda chipulumutso chanu

nthawi zonse anene kuti, "Mulungu akuzike!"

5 Koma ine ndine wosauka ndi wosowa;

bwerani msanga kwa ine Inu Mulungu.

Inu ndinu thandizo langa ndi momboli wanga;

Inu Yehova musachedwe.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-16_18-40-07-