Publicidade

Salmos 12

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe seminiti. Salimo la Davide.

1 Thandizeni Yehova pakuti palibe munthu wokhulupirika;

okhulupirika akusowa pakati pa anthu.

2 Aliyense amanamiza mʼbale wake;

ndi pakamwa pawo pabodza amayankhula zachinyengo.

3 Inu Yehova tsekani milomo yonse yachinyengo

ndi pakamwa paliponse podzikuza.

4 Pakamwa pamene pamati, "Ife tidzapambana ndi kuyankhula kwathu;

pakamwapa ndi pathupathu, tsono mbuye wathu ndani?"

5 "Chifukwa cha kuponderezedwa kwa anthu opanda mphamvu

ndi kubuwula kwa anthu osowa,

Ine ndidzauka tsopano," akutero Yehova,

"Ndidzawateteza kwa owazunza."

6 Ndipo mawu a Yehova ndi angwiro

monga siliva oyengedwa mʼngʼanjo yadothi,

oyengedwa kasanu nʼkawiri.

7 Inu Yehova mudzatitchinjiriza ndipo

mudzatiteteza kwa anthu otere kwamuyaya.

8 Oyipa amangoyendayenda ponseponse

anthu akamayamikira zochita zawo.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-15_21-32-39-