Publicidade

Salmos 87

Salimo la Ana a Kora.

1 Iye wakhazikitsa maziko ake pa phiri loyera;

2 Yehova amakonda zipata za Ziyoni

kupambana malo onse okhalamo a Yakobo.

3 Za ulemerero wako zimakambidwa,

Iwe mzinda wa Mulungu:

Sela

4 "Ndidzanena za Rahabe ndi Babuloni

pakati pa iwo amene amandidziwa.

Dzikonso la Filisitiya, Turo pamodzi ndi Kusi,

ndipo ndidzati, ‘Uyu anabadwira mʼZiyoni.’ "

5 Ndithudi, za Ziyoni adzanena kuti,

"Uyu ndi uyo anabadwira mwa iye,

ndipo Wammwambamwamba adzakhazikitsa iyeyo."

6 Yehova adzalemba mʼbuku la kawundula wa anthu a mitundu ina:

"Uyu anabadwira mʼZiyoni."

Sela

7 Oyimba ndi ovina omwe adzati,

"Akasupe anga onse ali mwa iwe."

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-15_21-32-39-