Pular para o conteúdo
Publicidade

YOSWA 12

Mayina a Mafumu Ogonjetsedwa

1 Aisraeli anagonjetsa dziko lonse la kummawa kwa Yorodani, kuyambira ku chigwa cha Arinoni mpaka ku phiri la Herimoni pamodzi ndi dera lonse la kummawa kwa Araba. Iwo anatenga dzikoli kukhala lawo, ndipo mafumu a dzikoli anali awa:

2 Sihoni mfumu ya Aamori,

amene ankakhala mu Hesiboni. Iye analamulira kuyambira ku Aroeri mzinda umene uli mʼmphepete mwa mtsinje wa Arinoni, mpaka ku mtsinje wa Yaboki, umene uli mʼmalire mwa Aamori, kuphatikizanso theka la dziko la Giliyadi. 3 Iye ankalamuliranso dera la chigwa cha Yorodani kuyambira ku Nyanja ya Kinereti, kummawa ndi kumatsika mpaka ku Beti-Yesimoti, mzinda umene unali kummawa kwa Nyanja ya Mchere ndi kutsikabe kummwera mpaka pa tsinde pa phiri la Pisiga.

4 Ogi mfumu ya mzinda wa Basani,

amene anali mmodzi mwa otsala mwa Arefaimu. Iye ankakhala ku Asiteroti ndi Ederi. 5 Dera la ufumu wake linafika ku phiri la Herimoni, ku Saleka ndi dziko lonse la Basani mpaka ku malire ndi anthu a ku Gesuri Makati. Ufumu wake unaphatikizanso theka la Giliyadi mpaka ku malire a mfumu Sihoni ya ku Hesiboni.

6 Mose mtumiki wa Yehova ndi Aisraeli anawagonjetsa ndipo anapereka dziko lawo kwa anthu a fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti chikhale cholowa chawo.

7 Yoswa ndi Aisraeli onse anagonjetsa mafumu onse okhala kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodani kuyambira ku Baala-Gadi, ku chigwa cha Lebanoni mpaka ku phiri la Halaki, kumapita cha ku Seiri. Yoswa anagawira dzikolo mafuko a Israeli kuti likhale cholowa chawo. 8 Dziko limeneli linali dera la ku mapiri, chigwa cha kumadzulo, chigwa cha Yorodani, ku matsitso a kummawa, ndi dziko la chipululu la kummwera. Amene ankakhala mʼdzikoli anali Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Mafumu ake anali awa:

9 mfumu ya Yeriko imodzi

mfumu ya Ai (kufupi ndi Beteli imodzi

10 mfumu ya Yerusalemu imodzi

mfumu ya Hebroni imodzi

11 mfumu ya Yarimuti imodzi

mfumu ya Lakisi imodzi

12 mfumu ya Egiloni imodzi

mfumu ya Gezeri imodzi

13 mfumu ya Debri imodzi

mfumu ya Gederi imodzi

14 mfumu ya Horima imodzi

mfumu ya Aradi imodzi

15 mfumu ya Libina imodzi

mfumu ya Adulamu imodzi

16 mfumu ya Makeda imodzi

mfumu ya Beteli imodzi

17 mfumu ya Tapuwa imodzi

mfumu ya Heferi imodzi

18 mfumu ya Afeki imodzi

mfumu ya Lasaroni imodzi

19 mfumu ya Madoni imodzi

mfumu ya Hazori imodzi

20 mfumu ya Simuroni Meroni imodzi

mfumu ya Akisafu imodzi

21 mfumu ya Taanaki imodzi

mfumu ya Megido imodzi

22 mfumu ya Kadesi imodzi

mfumu ya Yokineamu ku Karimeli imodzi

23 mfumu ya Dori ku Nafoti Dori imodzi

mfumu ya Goyini ku Giligala imodzi

24 mfumu ya Tiriza imodzi

  mafumu onse pamodzi analipo 31.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também