Publicidade

Cânticos 8

1 Ukanakhala kuti ndiwe mlongo wanga,

amene anayamwa mawere a amayi anga!

Ndikanakumana nawe pa njira,

ndikanakupsompsona,

ndipo palibe wina aliyense akanandinyoza.

2 Ndikanakutenga

ndi kukulowetsa mʼnyumba ya amayi anga,

amayi amene anandiphunzitsa,

ndikanakupatsa vinyo wotsekemera kuti umwe,

zotsekemera za makangadza.

3 Mutu wanga watsamira dzanja lake lamanzere

ndipo dzanja lake lamanja landikumbatira.

4 Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphani:

musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsa

mpaka pamene chifunire ichocho.

Abwenzi

5 Kodi ndani uyo akutuluka ku chipululuyo,

atatsamira wokondedwa wakeyo?

Mkazi

Ndinakudzutsa pa tsinde pa mtengo wa apulosi,

pamenepo ndi pamene amayi anachirira,

pamenepo ndi pamene wokubereka anamva ululu pokubala iweyo.

6 Undiyike pamtima pako ngati chidindo,

ngati chidindo cha pa dzanja lako;

pakuti chikondi nʼchamphamvu ngati imfa,

nsanje ndiyaliwuma ngati manda.

Chikondi chimachita kuti lawilawi

ngati malawi a moto wamphamvu.

7 Madzi ochuluka sangachizimitse chikondi,

mitsinje singachikokolole chikondicho.

Ngati wina apereka chuma chonse

cha mʼnyumba mwake chifukwa cha chikondi,

adzangonyozeka nazo kotheratu.

Abwenzi

8 Ife tili naye mlongo wathu wamngʼono,

koma alibe mawere,

kodi tidzamuchitira chiyani mlongo wathuyu

pa tsiku limene adzamufunsire?

9 Ngati iye ndi khoma,

tidzamumangira nsanja ya siliva.

Ngati iye ndi chitseko,

tidzamutchinga ndi matabwa a mkungudza.

Mkazi

10 Ine ndili ngati khoma,

ndipo mawere anga ndi nsanja zake.

Tsono mʼmaso mwa bwenzi langa

ndine wobweretsa mtendere.

11 Solomoni anali ndi munda wampesa ku Baala-Hamoni;

iyeyo anabwereketsa munda wamphesawo kwa alimi,

aliyense mwa iwo ankayenera kupereka

ndalama zasiliva 1,000 mʼmalo mwa zipatso zake.

12 Koma munda wanga wampesa ndi wangawanga ndiponso wa ine ndekha.

Iwe Solomoni, khala nazo ndalama zasiliva 1,000

ndipo ndalama zasiliva 200 ndi za amene akusamalira mundawo.

Mwamuna

13 Iwe amene umakhala mʼminda

uli pamodzi ndi anzako,

ndilole kuti ndimve liwu lako!

Mkazi

14 Fulumira wokondedwa wanga,

ndipo ukhale ngati gwape

kapena mwana wa mbawala

wothamanga mʼmapiri mʼmene mumamera mbewu zokometsera chakudya.

Veja também

Publicidade
Cânticos
Ver todos os capítulos de Cânticos
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-15_21-32-39-