Publicidade

Cânticos 6

Abwenzi

1 Iwe wokongola kuposa akazi onsewa,

kodi wokondedwa wakoyo wapita kuti?

Kodi wokondedwa wakoyo wakhotera njira iti

kuti timufunefune pamodzi ndi iwe?

Mkazi

2 Wachikondi wanga watsikira ku munda kwake,

ku timinda ta zokometsera zakudya,

akukadyetsa ziweto zake ku minda,

ndiponso akuthyola maluwa okongola.

3 Wokondedwa wangayo ndine wake ndipo iyeyo ndi wangawanga;

amadyetsa ziweto zake pakati pa maluwa okongola.

Mwamuna

4 Ndiwe wokongola, bwenzi langa, ngati Tiriza,

wokongola kwambiri ngati Yerusalemu,

ndiwe woopsa ngati gulu lankhondo lonyamula mbendera.

5 Usandipenyetsetse;

pakuti maso ako amanditenga mtima.

Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuzi

zikutsetsereka kuchokera ku Giliyadi.

6 Mano ako ali ngati gulu la nkhosa

zimene zikubwera kuchokera kokazisambitsa,

iliyonse ili ndi ana amapasa,

palibe imene ili yokha.

7 Kukhalira kumbuyo kwa nsalu yako yophimba kumutu,

masaya ako ali ngati mabandu a makangadza.

8 Ngakhale patakhala akazi a mfumu 60,

ndi azikazi 80,

ndi anamwali osawerengeka;

9 koma nkhunda yanga, wangwiro wanga ndi wosiyana ndi wina aliyense;

mwana wamkazi yekhayo wa amayi ake,

mwana wapamtima wa amene anamubereka.

Anamwali anamuona ndipo anamutcha wodala;

akazi a mfumu ndi azikazi anamutamanda.

Abwenzi

10 Ndani uyu akuoneka ngati mʼbandakucha,

wokongola ngati mwezi, wowala ngati dzuwa,

wochititsa mantha ngati gulu la ankhondo mbendera zili mʼmanja?

Mwamuna

11 Ndinatsikira ku munda wa mitengo ya alimondi

kukayangʼana zomera zatsopano ku chigwa,

kukaona ngati mpesa waphukira

kapena ngati makangadza ali ndi maluwa.

12 Ndisanazindikire kanthu,

ndinakhala ngati ndikulota kuti ndili mʼgaleta pambali pa mfumu yanga.

Abwenzi

13 Bwerera, bwerera iwe namwali wa ku Sulami;

bwerera, bwerera kuti ife tidzakupenyetsetse iwe!

Mwamuna

Chifukwa chiyani mukufuna kudzapenyetsetsa ine mwana wamkazi wa ku Sulami,

pamene ndikuvina pakati pa magulu awiri?

Veja também

Publicidade
Cânticos
Ver todos os capítulos de Cânticos
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-15_21-32-39-