Amor de casal
O amor de casal é celebrado na Bíblia como dom sagrado. O Cântico dos Cânticos exalta a beleza do amor conjugal — íntimo, exclusivo e forte como a morte.
Undiyike pamtima pako ngati chidindo,
ngati chidindo cha pa dzanja lako;
pakuti chikondi nʼchamphamvu ngati imfa,
nsanje ndiyaliwuma ngati manda.
Chikondi chimachita kuti lawilawi
ngati malawi a moto wamphamvu.
Madzi ochuluka sangachizimitse chikondi,
mitsinje singachikokolole chikondicho.
Ngati wina apereka chuma chonse
cha mʼnyumba mwake chifukwa cha chikondi,
adzangonyozeka nazo kotheratu.
Abwenzi
Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, wanditenga mtima,
iwe wanditenga mtima
ndi kapenyedwe ka maso ako,
ndiponso ndi umodzi mwa mikanda ya mʼkhosi mwako.
Undipsompsone ndi milomo yako
chifukwa chikondi chako nʼchokoma kuposa vinyo.
Mafuta ako odzola ndi onunkhira bwino;
dzina lako lili ngati mafuta onunkhira otsanulidwa.
Nʼchifukwa chake atsikana amakukonda!
Iwe wokondedwa wanga, ndiwe wokongoladi!
Ndithu, ndiwe chiphadzuwa,
maso ako ali ngati nkhunda.
Mkazi
Iwe bwenzi langa, ndiwe wokongoladi!
Ndithu, ndiwe wokongoladi kwambiri!
Ndipo malo athu ogonapo ndi msipu wobiriwira.
Mwamuna
Ndipo Yehova Mulungu anati, "Sibwino kuti munthu akhale yekha. Ndidzamupangira mnzake womuthandiza."
Motero Yehova Mulungu anapanga mkazi ndi nthiti ija imene anatenga kwa munthu uja nabwera naye kwa iye.
Munthu uja anati,
"Uyu ndiye fupa lochokera ku mafupa anga
ndi mnofu wochokera ku mnofu wanga;
adzatchedwa ‘mkazi,’
popeza wachokera mwa mwamuna."
Nʼchifukwa chake, mwamuna amasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake ndipo awiriwo amakhala thupi limodzi.
Wapeza mkazi wapeza chinthu chabwino
ndipo Yehova amamukomera mtima.
Yehova adalitse kasupe wako,
ndipo usangalale ndi mkazi wa unyamata wako.
Iye uja ali ngati mbalale yayikazi yokongola ndiponso ngati gwape wa maonekedwe abwino.
Ukhutitsidwe ndi mawere ake nthawi zonse,
ndipo utengeke ndi chikondi chake nthawi zonse.
Mwana wanga, nʼchifukwa chiyani ukukopeka ndi mkazi wachigololo?
Bwanji ukukumbatira mkazi wachilendo?
Motero salinso awiri ayi koma mmodzi. Nʼchifukwa chake chimene Mulungu wachimanga pamodzi munthu wina asachilekanitse."
Chikondi nʼcholeza mtima, chikondi nʼchokoma mtima, chilibe nsanje, sichidzikuza, sichidzitamandira. Chikondi chilibe mwano, sichodzikonda, sichipsa mtima msanga, sichisunga mangawa. Chikondi sichikondwera ndi zoyipa koma chimakondwera ndi choonadi. Chimatchinjiriza nthawi zonse, chimakhulupirika nthawi zonse, chimakhala ndi chiyembekezo nthawi zonse, chimapirira nthawi zonse.
Momwemonso, amuna akuyenera kukonda akazi awo monga matupi awo. Iye amene akonda mkazi wake adzikondanso yekha. Pakuti palibe amene amadana nalo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulisamalira bwino, monga momwe Khristu amachitira ndi mpingo wake
Chomwecho, aliyense mwa inu akuyenera kukonda mkazi wake monga adzikondera iye mwini, ndipo mkazi akuyenera kulemekeza mwamuna wake.
Ndipo kuwonjezera pa zonsezi valani chikondi, chimene chimangirira zonsezi pamodzi mu mgwirizano wangwiro.
Kukhala awiri nʼkwabwino kuposa kukhala wekha,
chifukwa ntchito ya anthu awiri ili ndi phindu:
Ngati winayo agwa,
mnzakeyo adzamudzutsa.
Koma tsoka kwa munthu amene agwa
ndipo alibe wina woti amudzutse!
Komanso ngati anthu awiri agona malo amodzi, adzafunditsana.
Koma nanga mmodzi angadzifunditse yekha?
Munthu mmodzi angathe kugonjetsedwa,
koma anthu awiri akhoza kudziteteza.
Chingwe cha maulusi atatu sichidukirapo.
Kodi Yehova sanawalenge iwo ngati munthu mmodzi? Ndi ake mʼthupi ndi mu mzimu. Nʼchifukwa chiyani ali mmodzi? Chifukwa Iye amafuna ana opembedza Mulungu. Motero samala moyo wako wauzimu, ndipo usakhale wosakhulupirika kwa mkazi wa unyamata wako.
Mwamuna akangokwatira kumene asamatumizidwe ku nkhondo kapena kupatsidwa ntchito ina iliyonse. Kwa chaka chathunthu akhale ndi ufulu wokhala pa khomo pake kumasangalatsa mkazi wakeyo.