Pular para o conteúdo
Publicidade

ZEKARIYA 3

Zovala Zoyera za Mkulu wa Ansembe

1 Pamenepo anandionetsa Yoswa, mkulu wa ansembe, atayima pamaso pa mngelo wa Yehova, ndipo Satana anayima ku dzanja lake lamanja kuti atsutsane naye. 2 Yehova anawuza Satana kuti, "Yehova akukudzudzula iwe Satana! Yehova amene wasankha Yerusalemu akukudzudzula! Kodi munthu uyu sali ngati chikuni choyaka chofumula pa moto?"

3 Tsono Yoswa anali atavala zovala zalitsiro pa nthawi imene anayima pamaso pa mngelo. 4 Mngelo uja anawuza anzake amene anali naye kuti, "Muvuleni zovala zake zalitsirizo."

Kenaka anawuza Yoswa kuti, "Taona, ndachotsa tchimo lako, ndipo ndikuveka zovala zokongola."

5 Ndipo ine ndinati, "Muvekeni nduwira yopatulika pamutu pake." Choncho anamuveka nduwira yopatulika pamutu pake, namuvekanso zovala zatsopano. Nthawiyi nʼkuti mngelo wa Yehova atayima pambali.

6 Mngelo wa Yehova analimbikitsa Yoswa kuti, 7 "Yehova Wamphamvuzonse akuti, Ngati uyenda mʼnjira zanga ndi kusunga malamulo anga, pamenepo udzalamulira nyumba yanga ndi kuyangʼanira mabwalo anga, ndipo ndidzakulolani kuti mudzakhale pamodzi ndi amene ali panowa.

8 " Mvera tsono, iwe Yoswa mkulu wa ansembe, pamodzi ndi anzako amene wakhala nawowa, amene ndi chizindikiro cha zinthu zimene zikubwera: Ine ndidzabweretsa mtumiki wanga, wotchedwa Nthambi. 9 Taona, mwala wokongola umene ndayika patsogolo pa Yoswa! Pa mwala umenewu pali maso asanu ndi awiri, ndipo Ine ndidzalembapo mawu,akutero Yehova Wamphamvuzonse, ndipo ndidzachotsa tchimo la dziko lino tsiku limodzi.

10 " Tsiku limenelo aliyense adzayitana mnzake kuti akhale pansi pa mtengo wamphesa ndi wa mkuyu,akutero Yehova Wamphamvuzonse."

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também