Pular para o conteúdo
Publicidade

ZEKARIYA 13

Kuyeretsedwa ku Tchimo

1 "Pa tsiku limenelo nyumba ya Davide adzayitsekulira kasupe wa madzi pamodzi ndi okhala mu Yerusalemu, kuti awachotsere tchimo lawo ndi chodetsa chawo.

2 "Pa tsiku limenelo, ndidzafafaniziratu mayina a mafano mʼdziko, ndipo sadzawakumbukiranso," akutero Yehova Wamphamvuzonse. "Ndidzachotsa mʼdziko aneneri pamodzi ndi mzimu wonyansa. 3 Ndipo ngati wina aliyense adzafuna kunenera, abambo ndi amayi ake amene anamubereka, adzamuwuza kuti, Uyenera kufa, chifukwa wayankhula bodza mʼdzina la Yehova.Pamene anenera, makolo ake omwe adzamubaya.

4 "Pa tsiku limenelo mneneri aliyense adzachita manyazi chifukwa cha masomphenya ake. Sadzavala chovala chake chaubweya ndi cholinga chonamiza anthu. 5 Iye adzati, Sindine mneneri. Ndine mlimi; ndakhala ndi kulima munda kuyambira ubwana wanga.6 Ngati wina adzamufunsa, Zilonda zili mʼthupi lakoli ndi chiyani?Iye adzayankha kuti, Zilondazi ndinazilandira mʼnyumba ya abwenzi anga.

Kukantha Mʼbusa, Nkhosa Kubalalika

7 "Dzambatuka iwe lupanga, ukanthe mʼbusa wanga,

ukanthe munthu amene ali pafupi ndi Ine!"

akutero Yehova Wamphamvuzonse.

Kantha mʼbusa

ndipo nkhosa zidzabalalika,

ndipo ndidzatambalitsa dzanja langa kuwononga zazingʼono.

8 Mʼdziko monse, akutero Yehova Wamphamvuzonse,

"zigawo ziwiri mwa zigawo zitatu za anthu zidzakanthidwa ndi kuwonongeka;

koma chigawo chimodzi chidzatsala mʼdzikomo.

9 Chigawo chachitatuchi ndidzachiyika pa moto;

ndidzawayeretsa monga momwe amayeretsera siliva

ndi kuwayesa monga momwe amayesera golide.

Adzayitana pa dzina langa

ndipo Ine ndidzawayankha;

Ine ndidzanena kuti, Awa ndi anthu anga,

ndipo iwo adzanena kuti, Yehova ndiye Mulungu wathu.’ "

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também