Ano novo
O Ano Novo é oportunidade de renovação e consagração. A Bíblia convida a esquecer o que ficou para trás e avançar em fé, confiança e esperança em Deus.
Abale, sindidziyesera ndekha kuti ndachipeza kale chimenechi. Koma chinthu chimodzi chimene ndimachita, nʼkuyiwala zamʼmbuyo ndi kuthamangira molimbika zinthu zimene zili mʼtsogolo mwanga. Ndikuthamangira kokathera mpikisanowo kuti ndikalandire mphotho imeneyi kumwamba, imene Mulungu anandiyitanira mwa Khristu Yesu.
Kuthamanga Mpaka Kumapeto pa Mpikisano wa Liwiro
Sikuti ndazipeza kale zonsezi, kapena kuti ndakhala kale wangwiro, koma ndikuthamangabe ndi kuyesetsa kuti ndipeze chimene Khristu Yesu anandiyitanira. Abale, sindidziyesera ndekha kuti ndachipeza kale chimenechi. Koma chinthu chimodzi chimene ndimachita, nʼkuyiwala zamʼmbuyo ndi kuthamangira molimbika zinthu zimene zili mʼtsogolo mwanga. Ndikuthamangira kokathera mpikisanowo kuti ndikalandire mphotho imeneyi kumwamba, imene Mulungu anandiyitanira mwa Khristu Yesu.
Kutsanzira Paulo
Choncho ife tonse amene tili okhwima pa moyo wauzimu, tikhale ndi maganizo omwewa. Ndipo ngati pena ndi pena muli ndi maganizo osiyana ndi amenewa, pameneponso Mulungu adzakuwunikirani.
Nʼchifukwa chake, ngati munthu aliyense ali mwa Khristu, ndi wolengedwa kwatsopano; zinthu zakale zapita taonani, zakhala zatsopano.
Kuyamika Mulungu Chifukwa cha Chiyembekezo Chamoyo
Alemekezedwe Mulungu, Atate wa Ambuye athu Yesu Khristu. Mwachifundo chake chachikulu anatibadwitsa kwatsopano, mʼchiyembekezo chamoyo pomuukitsa Yesu Khristu kwa akufa,
Mulenge mʼkati mwanga mtima woyera Inu Mulungu
ndi kukonzanso mzimu wokhazikika mwa ine.
Musandichotse pamaso panu
kapena kuchotsa Mzimu wanu Woyera mwa ine.
Khala chete pamaso pa Yehova ndipo umudikire mofatsa;
usavutike pamene anthu apambana mʼnjira zawo,
pamene iwo achita zinthu zawo zoyipa.
Lawani ndipo onani kuti Yehova ndi wabwino;
wodala munthu amene amathawira kwa Iye.
koma iwo amene amakhulupirira Yehova
adzalandira mphamvu zatsopano.
Adzawuluka ngati chiwombankhanga;
adzathamanga koma sadzalefuka,
adzayenda koma sadzatopa konse.
Pakuti Ine ndikudziwa zimene ndinakukonzerani," akutero Yehova, "ndimalingalira zabwino zokhazokha za inu osati zoyipa, ayi. Ndimalingalira zinthu zokupatsani chiyembekezo chenicheni pa za mʼtsogolo.
Ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera mtima. Zonse zimene zimakuyipitsani zidzachoka. Ndidzakuyeretsani pochotsa mafano anu onse. Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kulowetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzachotsa mwa inu mtima wanu wowuma ngati mwala ndi kukupatsani mtima wofewa ngati mnofu. Ndipo ndidzayika Mzimu wanga mwa inu ndipo ndidzakuthandizani kutsatira malangizo anga ndi kukusungitsani mosamala kwambiri malamulo anga.
Ndipo kuwonjezera pa zonsezi valani chikondi, chimene chimangirira zonsezi pamodzi mu mgwirizano wangwiro.
Mtendere wa Khristu ulamulire mʼmitima mwanu, popeza monga ziwalo za thupi limodzi, munayitanidwa kuti mukhale ndi mtendere. Ndipo muziyamika.
Iye anapanga chinthu chilichonse kuti chikhale chabwino pa nthawi yake. Anayika nzeru zamuyaya mʼmitima ya anthu; komabe anthuwo sangathe kuzindikira zomwe Mulungu wachita kuyambira pa chiyambi mpaka chimaliziro.
Abambo athu ankatilanga kwa kanthawi kochepa monga amaonera kufunika kwake, koma Mulungu amatilanga kuti tipindule, kuti tikhale oyera mtima. Palibe chilango chimene chimaoneka kuti ndi chabwino pa nthawiyo, komatu chowawa. Koma pambuyo pake, chimabweretsa chipatso chachilungamo ndi mtendere kwa iwo amene aleredwa mwa njira imeneyi.
Kunyadira za Mawa
Tsono tamverani, inu amene mumati, "Lero kapena mawa tipita ku mzinda wakutiwakuti, tikatha chaka chimodzi tikuchita malonda ndi kupanga ndalama." Chifukwa chiyani mukutero? Inu simukudziwa zimene ziti zichitike mawa. Kodi moyo wanu ndi wotani? Inu muli ngati nkhungu imene imangooneka kwa kanthawi kochepa ndipo kenaka ndikuzimirira. Koma inuyo muyenera kunena kuti, "Ambuye akalola, tikadzakhala ndi moyo, tidzachita zakutizakuti." Koma mmene zililimu mumangodzitama ndi kudzikuza. Kudzitama konse kotereku ndi koyipa. Aliyense amene amadziwa zabwino zimene amayenera kuchita koma osazichita, ndiye kuti wachimwa.