Arca de noé
A arca de Noé é história de salvação e fidelidade. Deus instruiu Noé a construir a arca para salvar sua família e os animais do dilúvio — exemplo supremo de obediência e fé.
Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, "Ndatsimikiza mtima kuti ndiwononge anthu onse, pakuti dziko lapansi ladzaza ndi ntchito zawo zoyipa. Ndithudi ndiwawononga pamodzi ndi zonse za pa dziko. Tsono udzipangire chombo cha matabwa a mtengo wanjale; mʼkati mwake upange zipinda ndipo upake phula mʼkati ndi kunja. Uchipange motere: Chombo chikhale mamita 140 mulitali, mamita 23 mulifupi ndi mamita 13 mu msinkhu wake. Uchipangire denga ndi kuchimaliza ndi zenera la masentimita makumi asanu. Uyike khomo mʼmbali mwa chombocho ndi kupanga zipinda zosanjikana; chapansi, chapakati ndi chapamwamba.
Ndipo Yehova anati kwa Nowa, "Lowa mu chombo iwe ndi banja lako lonse, chifukwa ndaona kuti ndiwe wolungama mu mʼbado uwu.
Ndipo Nowa, ana ake aamuna, mkazi wake, pamodzi ndi ana ake aakazi analowa mu chombo chija kuthawa madzi a chigumula. Nyama zoti nʼkudya ndi nyama zosadyedwa, mbalame, pamodzi ndi nyama zokwawa zonse zinadza kwa Nowa ziwiriziwiri ndi kulowa mʼchombomo. Ndipo Nowa anatenga ziwiriziwiri, yayimuna ndi yayikazi monga anamulamulira Mulungu. Patapita masiku asanu ndi awiri chigumula chinabwera pa dziko lapansi.
Iye analowa nazo zazimuna ndi zazikazi monga mmene Mulungu anamulamulira. Kenaka Yehova anatseka pa khomo.
Chigumula chinagwa pa dziko la pansi kwa masiku makumi anayi. Madzi anayamba kuchuluka ndipo ananyamula chombo chija ndi kuchiyandamitsa pamwamba pa dziko. Madzi anafika mwamphamvu ndipo anachulukirachulukira pa dziko lapansi moti chombo chinayandama pamwamba pa madziwo.
Chamoyo chilichonse pa dziko lapansi chinawonongedwa, kuyambira munthu, nyama, zokwawa ndi mbalame. Nowa yekha ndiye anatsala pamodzi ndi onse amene anali naye.
Madzi amaphwabe pa dziko lapansi. Pakutha pa masiku 150, madzi anatsika, ndipo pa tsiku la 17 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, chombo chija chinakakhazikika pa mapiri a Ararati.
Patapita masiku makumi anayi, Nowa anatsekula zenera limene anapanga mʼchombomo natulutsa khwangwala, koma khwangwalayo ankangowuluka uku ndi uku mpaka madzi anawuma pa dziko lapansi. Kenaka anatulutsa nkhunda kuti aone ngati madzi aphwa pa dziko. Koma nkhunda sinapeze poti nʼkutera chifukwa panali madzi ponseponse pa dziko lapansi. Choncho inabwerera kwa Nowa mʼchombo. Nowa anatulutsa dzanja lake kunja ndi kutenga nkhundayo kuyibwezera mʼchombo mmene iye anali. Choncho anadikirabe masiku ena asanu ndi awiri ndipo anatulutsanso nkhundayo mʼchombo muja. Pamene nkhunda inabwerera madzulo ake, inali itanyamula tsamba laliwisi la mtengo wa olivi. Motero Nowa anadziwa kuti madzi aphwadi pa dziko lapansi. Iye anadikira masiku ena asanu ndi awiri ndipo anatumizanso nkhunda ija, koma nthawi imeneyi sinabwererenso kwa iye.
Pofika tsiku loyamba la mwezi woyamba wa chaka chimene Nowa anakwanitsa zaka 601, madzi anawuma pa dziko lapansi. Ndipo Nowa anachotsa denga la chombo ndipo anaona kuti kunja kwawuma.
Tsono Mulungu anawuza Nowa kuti, "Iwe, mkazi wako, ana ako pamodzi ndi akazi awo tulukani mʼchombomo. Tulutsa zamoyo zonse zili ndi iwe, mbalame, nyama ndi zokwawa zonse kuti ziswane ndi kuchulukana pa dziko lapansi."
Mulungu anawuza Nowa ndi ana ake kuti, "Tsopano Ine ndapangana ndi iwe ndi zidzukulu zako zamʼtsogolomo, pamodzi ndi zamoyo zonse, mbalame, ziweto ndi nyama zonse za kuthengo, ndi zonse zimene zinatuluka mʼchombo pamodzi ndi iwe. Pangano langa ndi ili: Ine ndilonjeza kuti sindidzawononganso zamoyo ndi madzi a chigumula. Chigumula sichidzawononganso dziko lapansi."
Ndayika utawaleza wanga mʼmitambo, ndipo chidzakhala chizindikiro cha pangano langa ndi dziko lapansi.
Ndi chikhulupiriro, Nowa atachenjezedwa za zinthu zimene zinali zisanaoneke, anachita mantha napanga chombo kuti apulumutsire banja lake. Ndi chikhulupiriro chake anatsutsa dziko lapansi ndipo analandira chilungamo chimene chimabwera ndi chikhulupiriro.
ya anthu amene sanamvere Mulungu atadikira moleza mtima pa nthawi imene Nowa ankapanga chombo. Mʼchombo chija anthu owerengeka okha, asanu ndi atatu, ndiwo anapulumutsidwa ku madzi. Madziwo akufanizira ubatizo umene lero ukukupulumutsaninso, osati chifukwa chochotsa litsiro la mʼthupi koma chifukwa cha chikumbumtima choona pamaso pa Mulungu. Umakupulumutsani chifukwa cha kuuka kwa Yesu Khristu, amene anapita kumwamba ndipo ali kudzanja lamanja la Mulungu komwe angelo ndi maulamuliro ndi amphamvu amamvera Iye.
Monga momwe zinalili nthawi ya Nowa, momwemonso zidzatero pobwera kwa Mwana wa Munthu. Pakuti masiku amenewo chisanafike chigumula, anthu amadya ndi kumwa, kukwatira ndi kukwatiwa, mpaka tsiku limene Nowa analowa mʼchombo; ndipo sanadziwe za chimene chikanachitika mpaka pamene chigumula chinafika ndi kuwamiza onse. Umu ndi mmene zidzakhalira pobwera kwa Mwana wa Munthu. Amuna awiri adzakhala mʼmunda; wina adzatengedwa ndi wina adzatsala. Amayi awiri adzakhala akusinja pa mtondo; wina adzatengedwa ndi wina adzatsala.