Publicidade

Buscar a Deus

Por Bíblia Online

Buscar a Deus é o chamado mais urgente da Bíblia. Buscai primeiro o Reino de Deus. Os que buscam de todo coração encontram — porque Ele se deixa encontrar pelos que o procuram.

Buscai ao Senhor

Buscai ao Senhor enquanto se pode achar. Buscai e achareis. O Senhor recompensa os que o buscam com diligência.

Funafunani Yehova pamene Iye akupezeka.

Mupemphere kwa Iye pamene ali pafupi.

Funafunani Yehova pamene Iye akupezeka.

Mupemphere kwa Iye pamene ali pafupi.

Chiweruzo ndi Chipulumutso

"Ndinali wokonzeka kumva mapemphero a amene sankandipempha kanthu;

ndipo ndinalola kuti anthu amene ankandifunafuna kuti andipeze.

Kwa mtundu wa anthu umene sunkapempha chithandizo kwa Ine,

ndinati, Ine ndili pano, Ine ndili pano.

Iye amalimbitsa ofowoka

ndipo otopa amawawonjezera mphamvu.

Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufowoka,

ndipo achinyamata amapunthwa ndi kugwa;

koma iwo amene amakhulupirira Yehova

adzalandira mphamvu zatsopano.

Adzawuluka ngati chiwombankhanga;

adzathamanga koma sadzalefuka,

adzayenda koma sadzatopa konse.

Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;

funafunani nkhope yake nthawi zonse.

Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;

funafunani nkhope yake nthawi zonse.

"Ndipo iwe mwana wanga Solomoni, umvere Mulungu wa abambo ako, umutumikire ndi mtima wodzipereka kwathunthu ndi mtima wako wonse, pakuti Yehova amasanthula mtima wa aliyense, ndipo amadziwa maganizo aliwonse a munthu. Ngati ufunafuna Yehova, Iye adzapezeka; koma ngati umutaya, Iye adzakukana kwamuyaya.

ngati anthu anga, amene amatchedwa ndi dzina langa adzichepetsa ndi kupemphera ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zawo zoyipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwamba ndipo ndidzakhululuka tchimo lawo ndi kuchiritsa dziko lawo.

Iye anapita kukakumana ndi Asa ndipo anati kwa iye, "Tandimverani, inu Asa ndi Ayuda onse ndi Benjamini. Yehova ali ndi inu, inunso mukakhala naye. Ngati inu mumufunafuna Iye mudzamupeza, koma ngati mumusiya, Iye adzakusiyani.

Asa Akonza Chipembedzo

Mzimu wa Mulungu unabwera pa Azariya mwana wa Odedi. Iye anapita kukakumana ndi Asa ndipo anati kwa iye, "Tandimverani, inu Asa ndi Ayuda onse ndi Benjamini. Yehova ali ndi inu, inunso mukakhala naye. Ngati inu mumufunafuna Iye mudzamupeza, koma ngati mumusiya, Iye adzakusiyani. Kwa nthawi yayitali Israeli anali wopanda Mulungu weniweni, wopanda wansembe wophunzitsa ndi wopanda malamulo. Koma pamene anali pa mavuto anatembenukira kwa Yehova, Mulungu wa Israeli ndi kufunafuna Iye, ndipo anamupeza. Masiku amenewo sikunali kwabwino kuyenda ulendo, pakuti anthu onse okhala mʼdziko anali pa mavuto aakulu. Mtundu umodzi umakanthidwa ndi mtundu wina ndipo mzinda wina umakanthidwa ndi mzinda wina, pakuti Mulungu amawasautsa ndi mazunzo a mtundu uliwonse. Koma inu, khalani amphamvu ndipo musataye mtima, pakuti mudzalandira mphotho ya ntchito yanu."

Asa atamva mawu awa ndiponso uneneri wa Azariya mwana wa Odedi, analimba mtima. Iye anachotsa mafano onse onyansa mʼdziko lonse la Yuda ndi Benjamini ndi mʼmizinda yonse imene analanda a ku mapiri a Efereimu. Iye anakonzetsa guwa lansembe la Yehova limene linali kutsogolo kwa khonde la Nyumba ya Mulungu.

Kenaka anasonkhanitsa anthu onse a ku Yuda ndi Benjamini ndiponso anthu ochokera ku Efereimu, Manase ndi Simeoni amene ankakhala pakati pawo, pakuti gulu lalikulu linabwera kwa iye kuchokera ku Israeli litaona kuti anali ndi Yehova Mulungu wake.

Iwo anasonkhana mu Yerusalemu mwezi wachitatu wa chaka cha 15 cha ulamuliro wa Asa. Pa nthawi imeneyi anapereka nsembe kwa Yehova, ngʼombe 700 ndiponso nkhosa ndi mbuzi 7,000 zochokera pa zolanda ku nkhondo zimene anabweretsa. Iwo anachita pangano loti azifunafuna Yehova, Mulungu wa makolo awo, ndi mtima ndi moyo wawo wonse. Aliyense wosafunafuna Yehova Mulungu wa Israeli aziphedwa, kaya ndi wamngʼono kapena wamkulu, mwamuna kapena mkazi. Iwo analumbira kwa Yehova, mokweza mawu, akuyimba malipenga ndi mbetete. Anthu onse a ku Yuda anakondwera pa kulumbirako chifukwa analumbira ndi mtima wawo wonse. Iwo anafunafuna Mulungu mwachidwi, ndipo anamupeza Iye. Kotero Yehova anawapatsa mpumulo mbali zonse.

Mfumu Asa anachotsanso Maaka agogo ake pa udindo wa amayi a mfumu chifukwa anapanga fano lonyansa la Asera. Asa anagwetsa fanolo, naliswa ndipo kenaka anakaliwotcha ku chigwa cha Kidroni. Ngakhale kuti sanachotse malo opembedzerako mafano mu Israeli, mtima wa Asa unali wodzipereka kwathunthu kwa Yehova, masiku onse a moyo wake. Iye anabweretsanso mʼNyumba ya Mulungu zipangizo zasiliva, golide ndi ziwiya zina zimene iyeyo ndi abambo ake anazipatula.

Panalibenso nkhondo mpaka chaka cha 35 cha ufumu wa Asa.

De todo o coração

Buscar-me-eis e me achareis quando me buscardes de todo o coração. O Senhor é bom para os que o buscam.

Mudzandifunafuna ndipo mudzandipeza. Mukadzandifuna ndi mtima wanu wonse

Mudzandifunafuna ndipo mudzandipeza. Mukadzandifuna ndi mtima wanu wonse

Kodi suja mawu anga amatentha ngati moto? Suja mawu anga amaphwanya monga ichitira nyundo kuphwanya miyala?" Akutero Yehova.

Mukanali komweko, ngati mudzamufunafuna Yehova Mulungu wanu mudzamupeza koma ngati mutamufunafuna ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.

Odala ndi amene amasunga malamulo ake,

amene amafunafuna Iyeyo ndi mtima wawo wonse.

Odala ndi amene amasunga malamulo ake,

amene amafunafuna Iyeyo ndi mtima wawo wonse.

Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse;

musalole kuti ndisochere kuchoka pa malamulo anu.

Moyo wanga wafowoka ndi chisoni;

limbikitseni monga mwa mawu anu.

Ndidzayendayenda mwaufulu,

chifukwa ndinafunafuna malangizo anu.

Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;

funafunani nkhope yake nthawi yonse.

Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;

funafunani nkhope yake nthawi yonse.

Mtima wanga ukuti kwa Inu, "Funafuna nkhope yake!"

Nkhope yanu Yehova ndidzayifunafuna.

Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga,

moona mtima ine ndimakufunafunani;

moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu,

thupi langa likulakalaka inu,

mʼdziko lowuma ndi lotopetsa

kumene kulibe madzi.

Buscar e encontrar

Pedi e dar-se-vos-á. O Senhor está perto de todos os que o invocam em verdade. Quem o busca não ficará insatisfeito.

Pemphani, Funafunani, Gogodani

"Pemphani ndipo mudzapatsidwa; funafunani ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsekulirani.

"Choncho Ine ndikunena kwa inu kuti: Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza. Gogodani ndipo adzakutsekulirani. Pakuti aliyense amene amapempha amalandira. Munthu amene amafunafuna amapeza. Iye amene amagogoda amamutsekulira.

"Choncho Ine ndikunena kwa inu kuti: Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza. Gogodani ndipo adzakutsekulirani.

Koma funafunani ufumu wake, ndipo mudzapatsidwa zonsezi.

Pajatu Mwana wa Munthu anabwera kudzafunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho."

Iwo amene amadziwa dzina lanu adzadalira Inu,

pakuti Inu Yehova, simunawatayepo amene amafunafuna inu.

Iwo amene amadziwa dzina lanu adzadalira Inu,

pakuti Inu Yehova, simunawatayepo amene amafunafuna inu.

Ine ndinafunafuna Yehova ndipo Iye anandiyankha;

anandilanditsa ku mantha anga onse.

Mikango itha kulefuka ndi kumva njala

koma iwo amene amafunafuna Yehova sasowa kanthu kalikonse kabwino.

Udzikondweretse wekha mwa Yehova

ndipo Iye adzakupatsa zokhumba za mtima wako.

Yehova kumwamba wayangʼana pansi,

kuyangʼana anthu onse

kuti aone ngati alipo wina wanzeru,

amene amafunafuna Mulungu.

Inu Yehova, mwandisanthula

ndipo mukundidziwa.

Inu mumadziwa pamene ndikhala pansi ndi pamene ndidzuka;

mumazindikira maganizo anga muli kutali.

Iyeyo adzalandira madalitso kwa Yehova

ndipo Mulungu mpulumutsi wake adzagamula kuti alibe mlandu.

Umenewo ndiwo mʼbado wa amene amafunafuna Yehova;

amene amafunafuna nkhope yanu, Inu Mulungu wa Yakobo.

Sela

Força na busca

Buscai o bem e não o mal. Sede fortalecidos no Senhor. A busca por Deus traz renovação e plenitude de vida.

Zimene Yehova akunena kwa nyumba ya Israeli ndi izi:

"Mundifunefune kuti mukhale ndi moyo;

Zimene Yehova akunena kwa nyumba ya Israeli ndi izi:

"Mundifunefune kuti mukhale ndi moyo;

Muyike mtima wanu pa zabwino osati pa zoyipa,

kuti mukhale ndi moyo.

Mukatero Yehova Mulungu Wamphamvuzonse adzakhala nanu,

monga mmene mumanenera kuti ali nanu.

Ndikupemphera kuti kuchokera mʼchuma cha ulemerero wake alimbikitse moyo wanu wa mʼkati ndi mphamvu za Mzimu wake,

Zida Zankhondo za Mulungu

Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye ndi mwa mphamvu zake zazikulu.

Timapempheranso kuti Mulungu akulimbikitseni ndi mphamvu yake yonse ya ulemerero wake, kuti muzipirira zonse ndi mitima yofatsa ndi ya chimwemwe

Pakuti Mzimu amene Mulungu anatipatsa, si Mzimu wotipatsa manyazi, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzisunga.

Ndipo popanda chikhulupiriro nʼkosatheka kukondweretsa Mulungu, chifukwa aliyense amene amabwera kwa Iye ayenera kukhulupirira kuti Mulungu alipodi ndi kuti Iye amapereka mphotho kwa amene akumufunitsitsa.

Ndipo popanda chikhulupiriro nʼkosatheka kukondweretsa Mulungu, chifukwa aliyense amene amabwera kwa Iye ayenera kukhulupirira kuti Mulungu alipodi ndi kuti Iye amapereka mphotho kwa amene akumufunitsitsa.

Koma mudzalandira mphamvu Mzimu Woyera akadzafika pa inu; ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka ku malekezero a dziko lapansi."

Yehova akubwezere pa zimene wachitazi. Yehova Mulungu wa Israeli, amene wabwera pansi pa mapiko ake kuti akuteteze, akupatse mphotho yayikulu."

Tsono Mzimu wa Yehova unafika ndi mphamvu pa Samsoni ndipo ngakhale analibe chida mʼmanja mwake, iye anakadzula mkangowo ngati akukadzula mwana wambuzi. Koma sanawuze abambo kapena amayi ake zimene anachitazo.

Tsono Samsoni anapemphera kwa Yehova kuti, "Inu Yehova Ambuye anga, ndikumbukireni. Chonde ndilimbitseni nthawi yokha ino, inu Yehova, kuti ndiwabwezere Afilistiwa chifukwa cha maso anga awiri."

Nʼkwabwino kuthawira kwa Yehova

kusiyana ndi kudalira munthu.

Nʼkwabwino kuthawira kwa Yehova

kusiyana ndi kudalira mafumu.

Wapeza mkazi wapeza chinthu chabwino

ndipo Yehova amamukomera mtima.

Udziwe kuti nzeru ndi yoteronso pa moyo wako;

ngati uyipeza nzeruyo, zinthu zidzakuyendera bwino mʼtsogolo,

ndipo chiyembekezo chako sichidzapita pachabe.

Seja o primeiro
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-07-05_19-25-13-