Publicidade

Isaías 56

Chipulumutso kwa Anthu Ena Onse

1 Yehova akuti,

"Chitani chilungamo

ndi zinthu zabwino,

chifukwa chipulumutso changa chili pafupi

ndipo ndidzakuwombolani posachedwapa.

2 Ndi wodala munthu amene amachita zimenezi,

munthu amene amalimbika kuzichita,

amene amasunga Sabata osaliyipitsa,

ndipo amadziletsa kuchita zoyipa."

3 Mlendo amene waphatikana ndi Yehova asanene kuti,

"Ndithu Yehova wandichotsa pakati pa anthu ake."

Ndipo munthu wofulidwa asanene kuti,

"Ine ndine mtengo wowuma basi."

4 Popeza Yehova akuti,

"Wofulidwa amene amasunga masabata anga,

nachita zokomera Ine

ndi kusunga pangano langa,

5 ndidzawapatsa dzina ndi mbiri yabwino

mʼkati mwa Nyumba yanga ndi makoma ake,

kuposa kukhala ndi ana aamuna ndi aakazi.

Ndidzawapatsa dzina labwino,

losatha ndi losayiwalika."

6 Yehova akuti, "Alendo amene amadziphatika kwa Yehova,

motero kuti amamutumikira Iye,

amakonda dzina la Yehova,

amamugwirira ntchito,

komanso kusunga Sabata osaliyipitsa

ndi kusunga bwino pangano langa,

7 amenewa Ine ndidzawafikitsa ku phiri langa lopatulika,

ndidzawapatsa chimwemwe mʼnyumba yanga ya mapemphero.

Zopereka zawo zopsereza ndi nsembe zawo

ndidzazilandira pa guwa langa la nsembe.

Paja nyumba yanga idzatchedwa

nyumba ya mapemphero ya anthu a mitundu yonse."

8 Ambuye Yehova, amene amasonkhanitsa

Aisraeli onse ali ku ukapolo akunena kuti,

"Ndidzasonkhanitsano anthu ena

kuwonjezera amene anasonkhana kale."

Mulungu Adzazula Anthu Oyipa

9 Bwerani, inu zirombo zonse zakuthengo,

inu nonse zirombo zamʼnkhalango bwerani mudzadye!

10 Atsogoleri onse a Israeli ndi akhungu,

onse ndi opanda nzeru;

onse ndi agalu opanda mawu,

samatha kuwuwa:

amagona pansi nʼkumalota

amakonda kugona tulo.

11 Ali ngati agalu amene ali ndi njala yayikulu;

sakhuta konse.

Abusa nawonso samvetsa zinthu;

onse amachita monga akufunira,

aliyense amafunafuna zomupindulitsa iye mwini.

12 Aliyense amafuwulira mnzake kuti, "Bwera, tiye timwe vinyo!

Tiyeni timwe mowa mpaka kukhuta!

Mawa lidzakhala ngati leroli,

kapena kuposa lero lino."

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-16_06-50-08-