Publicidade

Isaías 28

Tsoka kwa Efereimu

1 Tsoka ufumu wonyada wa zidakwa za ku Efereimu.

Tsoka kwa ulemerero wake wokongola umene ukufota ngati duwa

limene lili pa mutu pa anthu

oledzera a mʼchigwa chachonde.

2 Taonani, ambuye ali naye wina wamphamvu ndi nyonga.

Iye adzabwera ngati mkuntho wamatalala ndi namondwe wowononga,

ngati madzi amphamvu osefukira a mvula yamkuntho;

ndipo adzawagwetsa pansi mwankhanza.

3 Ulamuliro wa atsogoleri oledzera

a ku Efereimu adzawuthetsa.

4 Ndipo ulemerero wokongola wa mzinda umene uli ngati duwa

lofota pamutu pa anthu oledzera a mʼchigwa chachonde uja,

udzakhala ngati nkhuyu yoyambirira kupsa

imene munthu akangoyiona amayithyola

nthawi yokolola isanakwane.

5 Tsiku limenelo Yehova Wamphamvuzonse

adzakhala ngati nkhata yaufumu,

chipewa chokongola

kwa anthu ake otsala.

6 Iye adzapereka mtima

wachilungamo kwa oweruza,

adzakhala chilimbikitso kwa

amene amabweza adani pa zipata za mzinda.

7 Nawonso awa ali dzandidzandi chifukwa cha vinyo

ndipo akusochera chifukwa cha mowa:

ansembe ndi aneneri akudzandira chifukwa cha mowa

ndipo akusokonezeka chifukwa cha vinyo;

akusochera chifukwa cha mowa,

akudzandira pamene akuona masomphenya,

kupunthwa pamene akupereka chigamulo.

8 Pa matebulo onse pali masanzi okhaokha

ndipo palibenso malo wopanda zonyansa.

9 Iwo akuti, "Kodi munthu ameneyu akufuna aphunzitse ndani?

Uthengawu akufuna kufotokozera yani?

Ndi kwa ana amene aleka kuyamwa,

kwa makanda ongowachotsa kumene ku bere?

10 Akuyesa kumatiphunzitsa pangʼonopangʼono

lemba ndi lemba, mzere ndi mzere,

phunziro ndi phunziro.

Zonsezi akungoti apa pangʼono apa pangʼono."

11 Mulungu adzayankhula kwa anthu ake kudzera mwa anthu aziyankhulo zachilendo, ziyankhulo zosamveka bwino.

Mulungu adzayankhula kwa anthu awa, amene

12 anakuwuzani kuti,

"Malo opumulira ndi ano,

otopa apumule, malo owusira ndi ano."

Koma inu simunamvere.

13 Choncho Yehova adzakuphunzitsani

pangʼonopangʼono lemba ndi lemba,

mzere ndi mzere, phunziro ndi phunziro.

Kotero mudzayenda ndi kugwa chambuyo,

adzapweteka ndi kukodwa mu msampha

ndipo adzakutengani ku ukapolo.

14 Nʼchifukwa chake imvani mawu a Yehova,

inu anthu achipongwe amene mumalamulira anthu awa mu Yerusalemu.

15 Inu mumayankhula monyada kuti, "Ife tinachita pangano ndi imfa,

ife tachita mgwirizano ndi manda.

Pamene mliri woopsa ukadzafika

sudzatikhudza ife,

chifukwa timadalira bodza ngati pothawirapo pathu

ndi chinyengo ngati malo anthu obisalapo."

16 Tsono zimene Ambuye Yehova akunena ndi izi:

"Taonani, ndikuyika mwala wovomerezeka ndi amisiri

ngati maziko mu Ziyoni,

mwala wapangodya, wamtengowapatali wopanga maziko amphamvu;

munthu amene awukhulupirira sadzagwedezeka.

17 Ntchito zolungama zidzakhala ngati chingwe choyezera maziko ake,

ndipo chilungamo chidzakhala chowongolera mzere;

matalala adzawononga malo anu othawirapo, amene ndi mabodza,

ndipo madzi adzamiza malo anu obisalako.

18 Pangano limene munachita ndi imfa lidzathetsedwa;

mgwirizano wanu ndi manda udzachotsedwa.

Pakuti mliri woopsa udzafika,

ndipo udzakugonjetsani.

19 Ndipo ukadzangofika udzakutengani.

Udzafika mmawa uliwonse,

usiku ndi usana."

Anthu akadzamvetsetsa uthenga umenewu

adzaopsedwa kwambiri.

20 Mudzakhala ngati munthu wogona pa bedi lalifupi kwambiri kuti sangathe kutambalitsapo miyendo;

ndiponso mudzakhala ngati munthu amene wafunda bulangeti lochepa kwambiri kuti sangathe nʼkufunda komwe.

21 Yehova adzamenya nkhondo monga anachitira ku phiri la Perazimu

adzakalipa monga anachitira ku chigwa cha Gibiyoni;

adzagwira ntchito yake yooneka ngati yachilendo,

ndipo zimene ati adzachite zidzakhala ngati zodabwitsa.

22 Tsopano lekani kunyoza,

mukapanda kutero maunyolo anu adzakuthinani kwambiri;

Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse wandiwuza kuti,

"Ndagamula kuti ndidzawononga dziko lapansi."

23 Tcherani khutu ndipo mumve mawu anga;

mvetserani ndipo mumve zimene ndikunena.

24 Kodi mlimi wofuna kudzala mbewu amangokhalira kutipula kokhakokha?

Kodi amangokhalira kugawula ndi kugalawuza kokhakokha?

25 Pamene iye wasalaza mundawo,

kodi samafesa mawere ndi chitowe?

Kodi suja samadzala tirigu

ndi barele mʼmizere yake,

nadzala mchewere mʼphepete mwa mundawo?

26 Mulungu wake amamulangiza

ndi kumuphunzitsa njira yabwino.

27 Mawere sapunthira chopunthira cha galeta lopanda mikombero,

kapena chitowe sapuntha popondetsapo mikombero ya galeta;

mawere amapuntha ndi ndodo

ndipo chitowe amapuntha ndi kamtengo.

28 Tirigu ayenera kusinjidwa kuti apangire buledi,

komabe munthu samangokhalira kupuntha tiriguyo osalekeza, kuopa kuti angatekedzeke.

Ngakhale kuti amapuntha tiriguyo poyendetsapo mikombero ya galeta,

koma akavalo ake satekedza tiriguyo.

29 Izinso zimachokera kwa Yehova Wamphamvuzonse,

wa uphungu wodabwitsa ndi wa nzeru zopambana.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-16_18-40-07-