Publicidade

Isaías 12

Nyimbo za Mayamiko

1 Tsiku limenelo aliyense wa inu adzati:

"Ndikukuyamikani, Inu Yehova;

chifukwa ngakhale munandipsera mtima,

mkwiyo wanu wachoka,

ndipo mwanditonthoza.

2 Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga;

ndidzamudalira ndipo sindidzachita mantha.

Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;

Iye wakhala chipulumutso changa."

3 Mudzakondwera popeza Yehova

ali ngati chitsime cha chipulumutso chanu.

4 Tsiku limenelo mudzati:

"Yamikani Yehova, tamandani dzina lake;

mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu,

ndipo mulalike kuti dzina lake ndi lopambana.

5 Imbirani Yehova, pakuti wachita ntchito zazikulu;

zimenezi zidziwike pa dziko lonse lapansi.

6 Fuwulani ndi kuyimba mwachimwemwe, inu anthu a ku Ziyoni;

pakuti Woyerayo wa Israeli ndi wamkulu pakati panu."

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-16_18-40-07-