Publicidade

Isaías 21

Za Chilango cha Babuloni

1 Uthenga wonena za chipululu cha mʼmbali mwa Nyanja.

Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya adzabwera ngati kamvuluvulu amene akuwomba modutsa mʼmbali ya nyanja,

kuchokera ku chipululu,

dziko lochititsa mantha.

2 Ine ndaona zinthu zoopsa mʼmasomphenya:

Wonyenga akunyenga, wofunkha akufunkha komanso owononga akuwononga.

Elamu, yambani nkhondo! Mediya, zingani mzinda!

Ine ndidzathetsa mavuto onse amene anayambitsa Ababuloni.

3 Chifukwa cha zimenezi thupi langa likunjenjemera ndi mantha,

ndikumva ululu ngati wa mayi amene akubereka;

ndikuvutika kwambiri ndi zimene ndikumva,

ndathedwa nzeru ndi zimene ndikuziona.

4 Mtima wanga ukugunda,

ndipo ndikunjenjemera ndi mantha;

chisisira chimene ndakhala ndikuchifuna

chasanduka chinthu choopsa kwa ine.

5 Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya akukonza matebulo,

akuyala mphasa,

akudya komanso kumwa!

Mwadzidzidzi anamva mawu akuti, "Dzukani inu ankhondo,

pakani mafuta zishango zanu!"

6 Zimene Ambuye akunena kwa ine ndi izi;

"Pita, kayike mlonda

kuti azinena zimene akuziona.

7 Taonani, anthu akubwera ali pa akavalo

ndipo akuyenda awiriawiri,

okwera pa bulu

kapena okwera pa ngamira,

mlondayo akhale tcheru kwambiri."

8 Ndipo mlondayo anafuwula kuti,

"Ambuye anga, tsiku ndi tsiku ndimakhala pa nsanja yolondera;

Usiku uliwonse ndimakhala pa malo anga olondera.

9 Taonani, uyo munthu akubwera atakwera pa galeta

ali ndi gulu la akavalo.

Mmodzi wa iwo akuti,

‘Babuloni wagwa, wagwa!

Mafano onse a milungu yake

agwa pansi ndipo aphwanyika!’ "

10 Inu anthu anga opunthidwa ndi kupetedwa ngati tirigu,

ine ndikukuwuzani zimene ndamva

ndikukuwuzani Uthenga wochokera kwa Yehova Wamphamvuzonse,

Mulungu wa Israeli.

Za Chilango cha Edomu

11 Uthenga wonena za Duma:

Munthu wina akundiyitana kuchokera ku Seiri kuti,

"Iwe mlonda, usikuwu utha liti?

Iwe mlonda, utha liti kodi usikuwu?"

12 Mlonda akuyankha kuti,

"Kukucha, koma kudanso.

Ngati ukufuna kufunsa, funsa tsopano;

ndipo ubwerenso udzafunse."

Za Chilango cha Arabiya

13 Uthenga wonena za Arabiya:

Inu anthu amalonda a ku Dedani,

amene usiku mumagona mʼzithukuluzi za ku Arabiya,

14 perekani madzi kwa anthu aludzu.

Inu anthu a ku Tema

perekani chakudya kwa anthu othawa nkhondo.

15 Iwo akuthawa malupanga,

lupanga losololedwa,

akuthawa uta wokokakoka

ndiponso nkhondo yoopsa.

16 Zimene Ambuye akunena kwa ine ndi izi: "Chaka chimodzi chisanathe, potsata mmene amawerengera munthu waganyu, ulemerero wonse wa Kedara udzatheratu. 17 Mwa anthu okoka uta, ankhondo a ku Kedara opulumuka adzakhala owerengeka." Wayankhula ndi Yehova Mulungu wa Israeli.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-15_21-32-39-