Publicidade

Coragem

Por Bíblia Online

A coragem cristã não é ausência de medo — é confiança em Deus maior que todo temor. Sê forte e corajoso! é o chamado repetido do Senhor aos seus filhos.

Sê forte e corajoso

O Senhor é a minha luz e a minha salvação — de quem terei medo? Com coragem enfrentamos o mundo, porque Deus está conosco.

Paja ndinakulamula kuti ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima. Choncho usamachite mantha kapena kutaya mtima popeza Ine Yehova Mulungu wako ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite."

Paja ndinakulamula kuti ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima. Choncho usamachite mantha kapena kutaya mtima popeza Ine Yehova Mulungu wako ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite."

Khalani amphamvu ndi olimba mtima. Musachite nawo mantha kapena kunjenjemera pamaso pawo, chifukwa Yehova Mulungu wanu apita nanu. Sadzakusiyani kapena kukutayani."

Khalani amphamvu ndi olimba mtima. Musachite nawo mantha kapena kunjenjemera pamaso pawo, chifukwa Yehova Mulungu wanu apita nanu. Sadzakusiyani kapena kukutayani."

Yehova mwini ndiye akukutsogolerani ndipo adzakhala nanu. Sadzakusiyani kapena kukutayani. Usachite mantha ndiponso usataye mtima."

Davide anatinso kwa mwana wake Solomoni, "Khala wamphamvu ndi wolimba mtima ndipo uchite ntchitoyi. Usachite mantha kapena kutaya mtima pakuti Yehova Mulungu wanga ali nawe. Iye sadzakukhumudwitsa kapena kukusiya mpaka ntchito yonse ya Nyumba ya Mulungu itatha.

Coragem em Cristo

Não vos deu Deus espírito de covardia. Sede fortes na fé! O perfeito amor lança fora todo medo.

Pakuti Mzimu amene Mulungu anatipatsa, si Mzimu wotipatsa manyazi, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzisunga.

Pakuti Mzimu amene Mulungu anatipatsa, si Mzimu wotipatsa manyazi, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzisunga.

Khalani tcheru; khazikikani mʼchikhulupiriro chanu; limbani mtima; khalani amphamvu.

Khalani tcheru; khazikikani mʼchikhulupiriro chanu; limbani mtima; khalani amphamvu.

Mulibe mantha mʼchikondi. Koma chikondi ndi changwiro chimachotsa mantha, chifukwa mantha amabwera chifukwa choopa chilango. Munthu amene ali ndi mantha, chikondi chake sichangwiro.

osachita mantha ndi pangʼono pomwe ndi amene akutsutsana nanu. Ichi ndi chizindikiro kwa iwo kuti adzawonongedwa, koma inu mudzapulumutsidwa ndi Mulungu.

Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu.

Mzimu amene inu munalandira samakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha, koma Mzimu amakusandutsani ana. Ndipo mwa Iye ife timafuwula kuti, "Abba, Atate."

Não temas

Não temas, porque Eu sou contigo. Quando tiver medo, em ti confiarei. Deus é nosso escudo e fortaleza.

Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe;

usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako.

Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza,

ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

Pakuti Ine Yehova, ndine Mulungu wako,

amene ndikukugwira dzanja lako lamanja

ndipo ndikuti, usaope;

ndidzakuthandiza.

Usachite mantha, pakuti Ine ndili nawe;

ndidzabweretsa ana ako kuchokera kummawa,

ndipo ndidzakusonkhanitsani kuchokera kumadzulo.

"Usachite mantha; sadzakunyozanso.

Usakhumudwe; sudzapeputsidwanso.

Udzayiwala za manyazi zimene zinakuchitikira nthawi ya unyamata wako

ndipo za manyazi zimene zinakuchitikira pa nthawi ya umasiye wako sudzazikumbukanso.

Ndikachita mantha

ndimadalira Inu.

Mwa Mulungu, amene mawu ake ine ndimatamanda,

mwa Mulungu ine ndimadaliramo; sindidzachita mantha.

Kodi munthu amene amafa angandichite chiyani?

Yehova ndiye kuwunika kwanga ndi chipulumutso changa;

ndidzaopa yani?

Yehova ndi linga la moyo wanga;

ndidzachita mantha ndi yani?

Dikirani pa Yehova;

khalani anyonga ndipo limbani mtima

nimudikire Yehova.

Dikirani pa Yehova;

khalani anyonga ndipo limbani mtima

nimudikire Yehova.

Khalani ndi nyonga ndipo limbani mtima,

inu nonse amene mumayembekezera Yehova.

Ngakhale ndiyende

mʼchigwa cha mdima wakuda bii,

sindidzaopa choyipa,

pakuti Inu muli ndi ine;

chibonga chanu ndi ndodo yanu

zimanditonthoza.

Conforto e encorajamento

O Deus de toda consolação nos consola em todas as tribulações. Coragem não falta a quem descansa em Deus.

Alemekezeke Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, Atate achifundo chonse, Mulungu wachitonthozo chonse. Iye amatitonthoza ife mʼmavuto athu onse, kuti ifenso tithe kutonthoza amene ali pavuto lililonse ndi chitonthozo chimene ife tilandira kwa Mulungu.

Koma tili ndi chuma ichi mʼmbiya zadothi, kusonyeza kuti mphamvu yoposayi, imachokera kwa Mulungu osati kwa ife. Tapanikizika kwambiri mbali zonse koma osaphwanyika; tathedwa nzeru koma osataya mtima; tazunzidwa, koma osasiyidwa; takanthidwa, koma osawonongeka. Nthawi zonse tikuyenda nayo imfa ya Yesu mʼthupi mwathu, kuti moyo wake Yesu uwonekenso mʼthupi mwathu. Pakuti nthawi zonse, ngakhale tili ndi moyo, tikuperekedwa ku imfa chifukwa cha Yesu, kuti moyo wake wa Yesu uwonekenso mʼmatupi mwathu amene amafa.

Mtima wanu usakonde ndalama koma mukhutitsidwe ndi zimene muli nazo, chifukwa Mulungu anati,

"Sadzakusiyani,

kapena kukutayani konse."

Kotero ife tikunena molimba mtima kuti,

"Ambuye ndiye mthandizi wanga;

sindidzachita mantha. Munthu angandichitenji ine?"

Ndani angakuchitireni zoyipa ngati muchita changu kuchita zabwino? Koma ngakhale mumve zowawa chifukwa cha chilungamo, ndinu odala. "Musaope anthu, musachite mantha."

Ine ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Ine sindikukupatsani monga dziko lapansi limaperekera. Mtima wanu usavutike ndipo musachite mantha.

koma atamuona Iye akuyenda pa nyanja, anaganiza kuti anali mzukwa. Iwo anafuwula, pakuti onse anamuona ndipo anachita mantha.

Nthawi yomweyo Iye anawayankhula nati, "Limbani mtima! Ndine. Musachite mantha."

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-22_10-02-25-