Deus nunca falha
Deus nunca falha. Nenhuma de suas promessas vem ao chão. O que Ele prometeu, Ele cumprirá. A fidelidade de Deus é o fundamento inabalável da nossa fé.
Promessas cumpridas
Nenhuma boa palavra falhou de todas as promessas que Deus fez. Ele é fiel e verdadeiro em tudo o que diz.
"Aliyense wa inu akudziwa mu mtima mwake komanso mʼmoyo mwake kuti zabwino zonse zimene Yehova Mulungu wanu anakulonjezani zachitika. Palibe lonjezo ndi limodzi lomwe limene silinakwaniritsidwe.
Yehova anakwaniritsa zonse zimene analonjeza kwa Aisraeli.
"Atamandike Yehova, amene wapereka mpumulo kwa anthu ake Aisraeli monga momwe analonjezera. Palibe mawu ndi amodzi omwe amene anapita pachabe pa malonjezo ake onse abwino amene anawapereka kudzera mwa mtumiki wake Mose.
Mulungu si munthu kuti aname,
kapena mwana wa munthu kuti asinthe maganizo ake.
Kodi amayankhula koma osachita?
Kodi amalonjeza koma osakwaniritsa?
Koma chikonzero cha Yehova chimakhala mpaka muyaya,
zolinga za mu mtima mwake pa mibado yonse.
Fidelidade eterna
A Palavra do Senhor permanece para sempre. A tua palavra é muito pura e o teu servo a ama profundamente.
Kwezani maso anu mlengalenga,
yangʼanani pansi pa dziko;
mlengalenga udzazimirira ngati utsi,
dziko lapansi lidzatha ngati chovala
ndipo anthu ake adzafa ngati nsabwe.
Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka muyaya,
chilungamo changa chidzakhala cha nthawi zonse.
Mawu anu ndi woyera kwambiri
nʼchifukwa chake mtumiki wanune ndimawakonda.
Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya,
ndipo ulamuliro wanu ndi wosatha pa mibado yonse.
Yehova ndi wokhulupirika pa malonjezo ake onse
ndi wokonda zonse zimene Iye anazipanga.
Yehova amagwiriziza onse amene akugwa
ndipo amakweza onse otsitsidwa.
Yehova amene ali pakati pawo ndi wolungama;
Iye salakwa.
Tsiku ndi tsiku amaweruza molungama,
ndipo tsiku lililonse salephera,
komabe ochita zoyipa sachita manyazi nʼkomwe.
Pakuti masomphenyawa akudikira nthawi yake;
masomphenyawa akunena zamʼtsogolo
ndipo sizidzalephera kuchitika.
Ngakhale achedwe kukwaniritsidwa, uwayembekezere;
zidzachitika ndithu ndipo sadzachedwa.
Segurança em Deus
Todas as promessas de Deus são sim e amém em Cristo. Fiel é Aquele que prometeu — Ele jamais nos decepcionará.
Pakuti ngakhale malonjezo a Mulungu atachuluka chotani, onsewo ndi "Inde" mwa Khristu. Kotero kuti mwa Iye, ife timati "Ameni" kuchitira Mulungu ulemu. Tsono ndi Mulungu amene anachititsa kuti inu ndi ife tiyime molimba mwa Khristu. Anatidzoza ife, nayikanso Mzimu wake mʼmitima mwathu kutitsimikizira za mʼtsogolo.
Tiyeni tigwiritsitse mosagwedezeka zimene timaziyembekezera ndi kuzivomereza, pakuti amene anatilonjezayo ndi wokhulupirika.
Ndipo inunso pamene munamva mawu a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, munayikidwanso mwa Khristu. Mutakhulupirira, anakusindikizani chizindikiro pokupatsani Mzimu Woyera amene Iye analonjeza. Mzimu Woyerayo ndi chikole chotsimikizira kuti tidzalandira madalitso athu, ndipo kuti Mulungu anatiwombola kuti tikhale anthu ake. Iye anachita zimenezi kuti timuyamike ndi kumulemekeza.
Wodala ndi munthu amene amapirira mʼmayesero, chifukwa akapambana adzalandira chipewa cha ulemerero chimene Mulungu analonjeza anthu amene amamukonda.