Domínio próprio
O domínio próprio é fruto do Espírito e marca de maturidade espiritual. A Bíblia ensina que quem governa o próprio espírito é melhor do que quem conquista uma cidade.
Fruto do Espírito
O fruto do Espírito inclui domínio próprio. A graça de Deus nos ensina a viver de maneira sóbria e justa neste mundo.
Koma chipatso cha Mzimu Woyera ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndi kudziretsa. Palibe lamulo loletsa zimenezi.
Pakuti chisomo cha Mulungu chimene chimapulumutsa chaonekera kwa anthu onse. Chisomo chimatiphunzitsa kukana moyo osalemekeza Mulungu komanso zilakolako za dziko lapansi. Ndipo chimatiphunzitsa kukhala moyo odziletsa, olungama ndi opembedza Mulungu nthawi ino, pamene tikudikira chiyembekezo chodala; kuonekera kwa ulemerero wa Mulungu wathu wamkulu ndi Mpulumutsi, Yesu Khristu,
Pakuti Mzimu amene Mulungu anatipatsa, si Mzimu wotipatsa manyazi, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzisunga.
Choncho, chitani khama kuwonjezera moyo wabwino pa chikhulupiriro chanu, ndipo pa moyo wabwino muwonjezerepo nzeru. Pa nzeru muwonjezerepo kudziretsa, pa kudziretsa muwonjezerepo chipiriro, ndipo pa chipiriro muwonjezerepo khalidwe lolemekeza Mulungu. Pa khalidwe lolemekeza Mulungu muwonjezerepo chifundo cha ubale, pa chifundo cha ubale muwonjezerepo chikondi.
Governar a si mesmo
Melhor é o que domina o seu espírito do que o que toma uma cidade. A cidade sem muros é o homem sem domínio próprio.
Munthu wosapsa mtima msanga amaposa munthu wankhondo,
munthu wowugwira mtima wake amaposa amene amalanda mzinda.
Munthu amene samatha kudziretsa
ali ngati mzinda umene adani awuthyola ndi kuwusiya wopanda malinga.
Munthu wopusa amaonetsa mkwiyo wake,
koma munthu wanzeru amadzigwira.
Mawu akachuluka zolakwa sizisowa,
koma amene amasunga pakamwa pake ndi wanzeru.
Kufunika kwa Kudziretsa
Kodi simukudziwa kuti pa mpikisano wa liwiro onse amathamanga ndithu, koma mmodzi yekha ndiye amalandira mphotho? Motero thamangani kuti mupate mphotho. Aliyense wochita mpikisano amakonzekera mwamphamvu. Amachita izi kuti alandire mphotho yankhata yamaluwa yomwe imafota. Koma ife timachita izi kuti tilandire mphotho yosafota. Choncho sindithamanga monga wothamanga wopanda cholinga; komanso sindichita mpikisano wankhonya monga munthu amene amangomenya mophonya. Ine ndimazunza thupi langa ndi kulisandutsa kapolo kuti nditatha kulalikira ena, ineyo ndingadzapezeke wosayenera kulandira nawo mphotho.
Koma ngati sangathe kudziretsa, akwatire, popeza ndi bwino kukwatira kusiyana ndi kudzizunza ndi chilakolako.
Palibe mayesero amene mwakumana nawo oposa amene anthu ena onse anakumana nawo. Mulungu ngokhulupirika; sadzalola kuti inu muyesedwe koposa muyeso umene mutha kupirira. Koma pamene mwayesedwa, Iyenso adzakupatsani njira yopambanira mayeserowo.
Disciplina e vigilância
Sede sóbrios e vigilantes. O diabo anda em derredor como leão rugidor. A sobriedade nos protege e fortalece.
Khalani odziretsa ndi atcheru. Mdani wanu mdierekezi amayendayenda monga mkango wobangula kufunafuna wina kuti amumeze. Mukaneni iye, ndipo mukhazikike mʼchikhulupiriro, chifukwa mukudziwa kuti abale anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso akumva zowawa zomwezi.
Chimaliziro cha zinthu zonse chili pafupi. Choncho khalani maso ndi odziletsa kuti muthe kupemphera.
Moyo Watsopano
Popeza kuti Khristu anamva zowawa mʼthupi lake, mukhale nawonso mtima omwewo, chifukwa iye amene wamva zowawa mʼthupi lake walekana nawo uchimo. Chifukwa cha ichi, iwo sakhalanso moyo wawo akuchita zofuna za matupi awo, koma amachita chifuniro cha Mulungu. Pakuti mwataya kale nthawi yambiri mʼmbuyomu pochita zimene anthu osapembedza amachita, moyo wokhumba zonyansa, zilakolako zoyipa kuledzera, zochitika zoyipa za pa phwando, mapokoso ndi kupembedza mafano onyansa. Anthu osapembedza amadabwa pamene simuthamangira nawo kuchita zoyipitsitsazi, nʼchifukwa chake amakuchitani chipongwe. Koma adzafotokoza okha mlandu wawo kwa Mulungu amene wakonzeka kuweruza amoyo ndi akufa.
aliyense wa inu aphunzire kulamulira thupi lake mʼnjira yoyera ndi yaulemu, osati yotsata chilakolako chonyansa monga amachitira akunja, amene sadziwa Mulungu.
O senhorio de Cristo
Todo domínio pertence a Cristo. Ele é Senhor dos senhores e Rei dos reis — e nos capacita a viver em santidade.
Tamandani Yehova, ntchito yake yonse
kulikonse mu ulamuliro wake.
Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.
Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya,
ndipo ulamuliro wanu ndi wosatha pa mibado yonse.
Yehova ndi wokhulupirika pa malonjezo ake onse
ndi wokonda zonse zimene Iye anazipanga.
"Ndikuyangʼanabe zinthu mʼmasomphenya usiku, ndinaona wina ngati mwana wa munthu, akubwera ndi mitambo ya kumwamba. Anayandikira Mkulu Wachikhalire uja. Ena anamuperekeza kwa Iye. Anapatsidwa ulamuliro, ulemerero ndi mphamvu za ufumu kuti anthu a mitundu ina yonse, mayiko ndi anthu aziyankhulo zosiyanasiyana apembedze iye. Mphamvu zake ndi mphamvu zamuyaya zimene sizidzatha, ndipo ufumu wake sudzawonongeka konse.
Chandikomera kukuwuzani zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa zimene Mulungu Wammwambamwamba wandichitira.
Zizindikiro zake ndi zazikulu,
zozizwitsa zake ndi zamphamvu!
Ufumu wake ndi wamuyaya;
ulamuliro wake ndi wa mibadomibado.
Chifukwa mwana watibadwira,
mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife,
ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake.
Ndipo adzamutcha dzina lake lakuti
Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu,
Atate Amuyaya, ndi Mfumu ya Mtendere.
Ulamuliro ndi mtendere wake
zidzakhala zopanda malire.
Iye adzalamulira ufumu wake ali pa
mpando waufumu wa Davide,
ndipo adzawukhazikitsa ndi kuwuchirikiza
mwa chiweruzo cholungama ndi pochita zachilungamo
kuyambira nthawi imeneyo mpaka muyaya.
Ndi mtima wake wonse, Yehova Wamphamvuzonse
watsimikiza kuchita zimenezi.
Pakuti Iye anatipulumutsa ku ulamuliro wa mdima ndi kutibweretsa mu ufumu wa Mwana wake wokondedwa. Mwa Iyeyu ife tinawomboledwa ndi kukhululukidwa machimo.
imene inagwira ntchito pamene Mulungu anaukitsa Khristu kwa akufa, namukhazika Iye ku dzanja lake lamanja mʼdziko la kumwamba. Anamukhazika pamwamba pa ulamuliro onse ndi mafumu, mphamvu ndi ufumu, ndiponso pamwamba pa dzina lililonse limene angalitchule, osati nthawi ino yokha komanso imene ikubwerayo.
Koma ife ndife nzika za kumwamba ndipo tikudikirira mwachidwi Mpulumutsi wochokera kumeneko, Ambuye Yesu Khristu. Iyeyo, ndi mphamvu imene imamuthandiza kukhazikitsa zinthu zonse pansi pa ulamuliro wake, adzasintha matupi athu achabewa kuti akhale ofanana ndi thupi lake la ulemerero.
Pakuti tikudziwa kuti popeza Khristu anaukitsidwa kwa akufa, Iye sangafenso. Imfa ilibenso mphamvu pa Iye.
Ndipo anthu amene amalamulidwa ndi khalidwe lauchimo sangathe kukondweretsa Mulungu.
Koma inu simulamulidwanso ndi khalidwe lanu lauchimo koma ndi Mzimu ngati Mzimu wa Mulungu akhaladi mwa inu. Koma ngati munthu aliyense alibe Mzimu wa Khristu, iyeyu si wa Khristu.
Pakuti monga mwa Adamu onse amafa, chomwechonso mwa Khristu onse adzakhala ndi amoyo. Koma aliyense adzauka pa nthawi yake. Khristu ndiye woyambirira, pambuyo pake, pamene Khristu adzabwera, iwo amene ali ake adzauka. Pamenepo chimaliziro chidzafika, pamene Iye adzapereka ufumu kwa Mulungu Atate, atathetsa ufumu wonse, ulamuliro wonse ndi mphamvu zonse. Pakuti Iye ayenera kulamulira mpaka Mulungu atayika pansi pa mapazi ake adani ake onse.
"Ulamuliro ndi kuopsa ndi za Mulungu,
Iye amakhazikitsa bata mu ufumu wake kumwambako.