Família
A família é a primeira instituição criada por Deus. Ele a projetou para ser escola de amor, fé e formação de caráter. A Bíblia honra a família e nos ensina a cuidar dela.
Eu e minha casa
Eu e minha casa serviremos ao Senhor. A família que serve a Deus juntos permanece unida e fortalecida em todas as circunstâncias.
Koma ngati kutumikira Yehova kukuyipirani, sankhani lero amene mudzamutumikire, kapena milungu imene makolo anu ankayitumikira kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate, kapena milungu ya Aamori, amene mukukhala mʼdziko lawo. Koma ine ndi banja langa, tidzatumikira Yehova."
Koma ngati kutumikira Yehova kukuyipirani, sankhani lero amene mudzamutumikire, kapena milungu imene makolo anu ankayitumikira kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate, kapena milungu ya Aamori, amene mukukhala mʼdziko lawo. Koma ine ndi banja langa, tidzatumikira Yehova."
Iwo anayankha kuti, "Khulupirira Ambuye Yesu ndipo udzapulumuka, iwe ndi a mʼbanja lako."
Yehova Mulungu wathu akhale nafe monga momwe anakhalira ndi makolo athu; asatisiye kapena kutitaya.
Criar os filhos
Instrui a criança no caminho em que deve andar. O lar é a primeira escola de fé e obediência.
Mwana muzimuphunzitsa njira yake,
ndipo akadzakalamba sadzachokamo.
Mwana muzimuphunzitsa njira yake,
ndipo akadzakalamba sadzachokamo.
Malangizo kuti Asunge Nzeru
Malangizo kwa Achinyamata
Mwana wanga, mvera malangizo a abambo ako
ndipo usakane mawu okuwongolera a amayi ako.
Ali ngati sangamutu yokongola ya maluwa pamutu pako
ndiponso ali ngati mkanda mʼkhosi mwako.
Chenjezo pa za Chigololo
Mwana wanga, usunge malamulo a abambo ako;
ndipo usataye zimene anakuphunzitsa amayi ako.
Malamulo amene ndakupatsani lero ayenera kukhala mu mtima mwanu. Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu. Muzikamba za malamulowa pamene muli mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mukugona ndi pamene mukudzuka.
Malamulo amene ndakupatsani lero ayenera kukhala mu mtima mwanu. Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu. Muzikamba za malamulowa pamene muli mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mukugona ndi pamene mukudzuka.
Abambo musakwiyitse ana anu; mʼmalo mwake, muwalere mʼchiphunzitso ndi mʼchilangizo cha Ambuye.
Abambo musakwiyitse ana anu; mʼmalo mwake, muwalere mʼchiphunzitso ndi mʼchilangizo cha Ambuye.
Ana ndi Makolo Awo
Inu ana, mverani makolo anu mwa Ambuye, pakuti zimenezi ndi zoyenera. "Lemekeza abambo ndi amayi ako." Limeneli ndi lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo.
Honrar e amar
Honra teu pai e tua mãe. A família funciona com perdão, paciência e amor incondicional entre todos os seus membros.
"Lemekeza abambo ako ndi amayi ako kuti ukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.
"Lemekeza abambo ako ndi amayi ako kuti ukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.
lemekeza abambo ako ndi amayi ako ndipo konda mnansi wako monga iwe mwini."
Za Kuthetsa Ukwati
Yesu atatsiriza kunena zinthu zimenezi, anachoka ku Galileya ndi kupita ku chigawo cha Yudeya mbali ina ya mtsinje wa Yorodani. Magulu akulu a anthu anamutsatira Iye, ndipo iwo anachiritsidwa pomwepo.
Afarisi ena anabwera kwa Iye kudzamuyesa. Anamufunsa Iye nati, "Kodi ndikololedwa kuti mwamuna amuleke mkazi wake pa chifukwa china chilichonse?"
Iye anayankha kuti, "Kodi simunawerenge kuti pachiyambi Mulungu analenga iwo, ‘mwamuna ndi mkazi?’ Ndipo anati, ‘Pa chifukwa ichi mwamuna adzasiya abambo ake ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.’ Motero salinso awiri ayi koma mmodzi. Nʼchifukwa chake chimene Mulungu wachimanga pamodzi munthu wina asachilekanitse."
Ndipo iwo anamufunsa nati, "Nanga nʼchifukwa chiyani Mose analamula kuti mwamuna azipatsa mkazi wake kalata ya chisudzulo ndi kumuchotsa?"
Yesu anayankha kuti, "Mose anakulolezani kuti muzisudzula akazi anu chifukwa cha kuwuma mitima kwanu. Koma sizinali chotere kuyambira pachiyambi. Ine ndikuwuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chiwerewere nakakwatira mkazi wina, achita chigololo."
Ophunzira ake anati kwa Iye, "Ngati umu ndi mmene zilili pa mwamuna ndi mkazi, kuli bwino kusakwatira."
Yesu anayankha kuti, "Si aliyense amene angavomere chiphunzitso ichi, koma kwa okhawo amene achimvetsetsa. Pakuti ena ndi akuti sangakwatire chifukwa anabadwa motero, ena ali motero chifukwa chofulidwa ndi anthu ndipo ena anawukana ukwati chifukwa cha ufumu wakumwamba. Iye amene angalandire ichi alandire."
Yesu Adalitsa Ana
Pamenepo anabwera nawo ana kwa Yesu kuti awasanjike manja ndi kuwapempherera. Koma ophunzira ake anadzudzula amene anabweretsa anawo.
Yesu anati, "Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse pakuti ufumu wakumwamba ndi wa iwo onga anawa." Atasanjika manja ake pa anawo, anachokapo.
Mnyamata Wolemera ndi Ufumu wa Mulungu
Taonani mnyamata wina anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, "Aphunzitsi, ndi chinthu chiti chabwino chimene ndiyenera kuchita kuti ndipeze moyo wosatha?"
Yesu anayankha kuti, "Ukundifunsiranji Ine za chinthu chimene ndi chabwino? Pali mmodzi yekha amene ndi wabwino. Ngati ukufuna kulowa mʼmoyo wosatha mvera malamulo."
Mnyamatayo anamufunsa kuti, "Ndi ati?"
Yesu anayankha kuti, "Usaphe, usachite chigololo, usabe, usapereke umboni onama, lemekeza abambo ako ndi amayi ako ndipo konda mnansi wako monga iwe mwini."
Mnyamatayo anati, "Zonsezi ndimazisunga, nanga chatsala ndi chiyani?"
Yesu anayankha kuti, "Ngati ukufuna kukhala wangwiro, pita kagulitse katundu wako ndi kupereka kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Ukakachita zimenezi, ukabwere udzanditsate Ine."
Mnyamatayo atamva zimenezi, anachoka mokhumudwa, chifukwa anali ndi chuma chambiri.
Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, "Zoonadi, ndikuwuzani kuti nʼkovuta kuti olemera akalowe mu ufumu wakumwamba. Komanso ndikuwuzani kuti, nʼkwapafupi kuti ngamira idzere pa kabowo ka zingano kusiyana ndi kuti wolemera akalowe mu ufumu wa Mulungu."
Ophunzira atamva zimenezi, anadabwa kwambiri ndipo anamufunsa kuti, "Nanga angapulumuke ndani?"
Yesu anawayangʼana iwo nati, "Ndi anthu, izi nʼzosatheka, koma ndi Mulungu zinthu zonse zimatheka."
Petro anamuyankha Iye kuti, "Ife tinasiya zonse ndi kukutsatirani Inu! Nanga tsono ife tidzalandira chiyani?"
Yesu anawawuza kuti, "Zoonadi, ndikuwuzani kuti pa nthawi yokonzanso zinthu zonse, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa mpando wake waufumu mu ulemerero wake kumwamba, inu amene mwanditsata Ine mudzakhalanso pa mipando khumi ndi iwiri yaufumu, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israeli. Ndipo aliyense amene wasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena bambo kapena mayi kapena mkazi, kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine adzalandira madalitso ochuluka ndi kulandiranso moyo wosatha. Koma ambiri amene ali oyambirira adzakhala omalizira, ndipo ambiri amene ndi omalizira adzakhala oyambirira."
Mukomerane mtima ndi kuchitirana chifundo wina ndi mnzake. Khululukiranani wina ndi mnzake, monga momwe Mulungu anakukhululukirani mwa Khristu.
Chomwecho, aliyense mwa inu akuyenera kukonda mkazi wake monga adzikondera iye mwini, ndipo mkazi akuyenera kulemekeza mwamuna wake.
Ngati wina anena kuti, "Ine ndimakonda Mulungu," koma namadana ndi mʼbale wake ndi wabodza ameneyo. Pakuti aliyense amene sakonda mʼbale wake, amene akumuona, sangathenso kukonda Mulungu amene sanamuone.
Cuidar da família
Quem não cuida dos seus negou a fé. A família é responsabilidade sagrada — prover, proteger e abençoar é mandamento divino.
Ngati wina sasamalira abale ake, makamaka a mʼbanja mwake mwenimweni, ameneyo wakana chikhulupiriro ndipo ndi woyipa kuposa wosakhulupirira.
Ngati wina sasamalira abale ake, makamaka a mʼbanja mwake mwenimweni, ameneyo wakana chikhulupiriro ndipo ndi woyipa kuposa wosakhulupirira.
Koma ngati mkazi wamasiye ali ndi ana ndi zidzukulu, anawo ayambe aphunzira kukwaniritsa udindo wawo pa banja lawo moopa Mulungu, potero akubweza zabwino kwa makolo awo ndi agogo awo. Pakuti zimenezi ndiye zimakondweretsa Mulungu.
Kugawikana mu Mpingo
Ndidandaulira inu, abale, mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu kuti nonsenu muvomerezane wina ndi mnzake kuti pasakhale kugawikana pakati panu ndi kuti mukhale amodzi kwenikweni mu nzeru ndi mʼmaganizo.
Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova,
ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.
Ana a pa unyamata ali ngati mivi mʼmanja
mwa munthu wankhondo.
Wodala munthu
amene motengera mivi mwake mwadzaza.
Iwo sadzachititsidwa manyazi
pamene alimbana ndi adani awo pa zipata.
Koma kuchokera muyaya mpaka muyaya
chikondi cha Yehova chili ndi iwo amene amamuopa,
ndi chilungamo chake chili ndi ana a ana awo;
iwo amene amasunga pangano lake
ndi kukumbukira kumvera malangizo ake.
Koma kuchokera muyaya mpaka muyaya
chikondi cha Yehova chili ndi iwo amene amamuopa,
ndi chilungamo chake chili ndi ana a ana awo;
iwo amene amasunga pangano lake
ndi kukumbukira kumvera malangizo ake.
Onani, nʼkokoma ndi kokondweretsa ndithu
pamene abale akhala pamodzi mwachiyanjano!
Unidade familiar
A coroa dos velhos são os filhos dos filhos. O casamento, os filhos e a comunhão familiar são bênçãos de Deus.
Zidzukulu ndiye ulemu wa anthu okalamba,
ndipo makolo ndiye ulemerero wa ana.
Zidzukulu ndiye ulemu wa anthu okalamba,
ndipo makolo ndiye ulemerero wa ana.
Bwenzi lako limakukonda nthawi zonse,
ndipo mʼbale wako anabadwa kuti azikuthandiza pamavuto.
Pali abwenzi amene chibwenzi chawo nʼchapamaso,
koma pali bwenzi limene limakukangamira kuposa mʼbale wako.
Usasiye bwenzi lako ndiponso bwenzi la abambo ako,
ndipo usapite ku nyumba ya mʼbale wako pamene wakumana ndi mavuto;
mnzako wokhala naye pafupi amaposa mʼbale wako wokhala kutali.
Mwana wanga, ngati mtima wako ukhala wanzeru,
inenso mtima wanga udzakondwera.
Abambo a munthu wolungama ali ndi chimwemwe chachikulu;
Wobala mwana wanzeru adzakondwera naye.
Miyambo ya Solomoni
Miyambo ya Solomoni:
Mwana wanzeru amakondweretsa abambo ake,
koma mwana wopusa amamvetsa amayi ake chisoni.
Ugwiriretu ntchito zako zonse,
makamaka za ku munda
ndipo pambuyo pake uyambe kumanga nyumba.
Munthu wofuna phindu mwachinyengo amavutitsa banja lake,
koma wodana ndi ziphuphu adzakhala ndi moyo.
Wovutitsa a mʼnyumba mwake adzalowa mʼmavuto,
ndipo chitsiru chidzakhala kapolo wa munthu wa nzeru.
Casamento e família
O homem deixará pai e mãe e se unirá à sua mulher. A família começa no casamento — aliança sagrada diante de Deus.
Nʼchifukwa chake, mwamuna amasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake ndipo awiriwo amakhala thupi limodzi.
Mulungu anawadalitsa nati kwa iwo, "Muberekane, muchulukane, mudzaze dziko lapansi ndipo muligonjetse. Mulamulire nsomba zamʼnyanja, mbalame zamlengalenga ndi cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimayenda mokwawa pa dziko lapansi."
Uzikondwerera moyo pamodzi ndi mkazi wako amene umamukonda, masiku onse a moyo uno wopanda phindu, amene Mulungu wakupatsa pansi pano. Pakuti mkaziyo ndiye gawo la moyo wako pa ntchito yako yolemetsa pansi pano.
Koma pachiyambi cha chilengedwe, Mulungu ‘analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.’ ‘Pa chifukwa ichi mwamuna adzasiya abambo ake ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.’ Potero sali awirinso, koma mmodzi. Chifukwa chake chimene Mulungu wachilumikiza pamodzi, munthu wina asachilekanitse."
Tsono ngati inu, anthu oyipa, mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, koposa kotani Atate anu akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene awapempha!"
"Kodi amayi angathe kuyiwala mwana wawo wakubere
ndi kusachitira chifundo mwana amene anabereka iwo eni?
Ngakhale iye angathe kuyiwala,
Ine sindidzakuyiwala iwe!
Taona, ndakulemba iwe mʼzikhantho zanga;
makoma ako ndimawaona nthawi zonse.
Abale okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Koma tikudziwa kuti Yesu akadzaonekera, tidzafanana naye, pakuti tidzamuona Iyeyo monga momwe alili. Aliyense amene ali ndi chiyembekezo ichi mwa Iye adziyeretse yekha, monga Iye ali woyera.