Misericórdia
A misericórdia de Deus é eterna e inesgotável. Ele se compadece dos que sofrem, perdoa os arrependidos e derrama graça sobre os que não merecem. Grande é a sua fidelidade.
A misericórdia de Deus
Quem é Deus como tu, que perdoa a iniquidade? Ele se deleita em ter misericórdia e não retém a ira para sempre.
Kodi alipo Mulungu wofanana nanu,
amene amakhululukira tchimo ndi kuyiwala zolakwa
za anthu otsala amene ndi cholowa chake?
Inu simusunga mkwiyo mpaka muyaya
koma kwanu nʼkuonetsa chikondi chosasinthika.
Mundichitire chifundo, Inu Mulungu,
molingana ndi chikondi chanu chosasinthika;
molingana ndi chifundo chanu chachikulu
mufafanize mphulupulu zanga.
Munditsuke zolakwa zanga zonse
ndipo mundiyeretse kuchotsa tchimo langa.
Kumbukirani Inu Yehova chifundo ndi chikondi chanu chachikulu,
pakuti ndi zakalekale.
Musakumbukire machimo a ubwana wanga
ndi makhalidwe anga owukira;
molingana ndi chikondi chanu ndikumbukireni ine,
pakuti Inu Yehova ndinu wabwino.
Ndikulirira kwa Inu Yehova ndili mʼdzenje lozama;
Ambuye imvani mawu anga.
Makutu anu akhale tcheru kumva
kupempha chifundo kwanga.
Musandichotsere chifundo chanu Yehova;
chikondi chanu ndi choonadi chanu zinditeteze nthawi zonse.
Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata
masiku onse a moyo wanga,
ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova
kwamuyaya.
Monga bambo amachitira chifundo ana ake,
choncho Yehova ali ndi chifundo ndi iwo amene amamuopa;
Graça e perdão
Onde o pecado abundou, superabundou a graça. Deus convida todos ao arrependimento e promete perdão total aos que confessam.
Koma sitingafananitse mphatso yaulereyo ndi kuchimwa kwa anthu. Pakuti ngati anthu ambiri anafa chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodziyo, kuli koposa bwanji nanga chisomo cha Mulungu ndi mphatso zomwe zinabwera ndi chisomo cha munthu mmodzi, Yesu Khristu, ndi kusefukira kwa ambiri!
Nʼchiyani tsono? Kodi tidzichimwa chifukwa sitikulamulidwa ndi Malamulo koma chisomo? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi!
Koma chifukwa cha chikondi chake chachikulu pa ife, Mulungu amene ndi olemera mʼchifundo, anatipanga kukhala amoyo ndi Khristu ngakhale pamene ife tinali akufa mu zolakwa zathu. Koma tinapulumutsidwa mwachisomo.
Koma anandiwuza kuti, "Chisomo changa ndi chokukwanira, pakuti mphamvu zanga zimaoneka kwathunthu mwa munthu wofowoka." Choncho ndidzadzitamandira mokondwera chifukwa cha zofowoka zanga, kuti mʼkutero mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.
Wobisa machimo ake sadzaona mwayi,
koma aliyense amene awulula ndi kuleka machimowo, adzalandira chifundo.
Woyipa asiye makhalidwe ake oyipa,
ndipo wosalungama asinthe maganizo ake oyipa.
Abwerere kwa Yehova, ndipo adzamuchitira chifundo,
ndi kwa Mulungu wathu, pakuti adzamukhululukira koposa.
Komatu Yehova akufunitsitsa kuti akukomereni mtima,
iye ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo.
Pakuti Yehova ndi Mulungu wachilungamo.
Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!
Misericórdia e compaixão
Misericórdia quero e não sacrifício. Deus nos chama a ser misericordiosos como Ele é, perdoando e acolhendo o próximo.
Koma pitani kaphunzireni tanthauzo la mawu awa: ‘Ndimafuna chifundo osati nsembe ayi.’ Pakuti sindinabwere kudzayitana olungama koma ochimwa."
Kenaka Petro anabwera kwa Yesu ndi kumufunsa kuti, "Ambuye, kodi mʼbale wanga akandichimwira ndimukhululukire kokwanira kangati? Mpaka kasanu nʼkawiri?"
Yesu anayankha kuti, "Ine ndikukuwuza iwe kuti osati kasanu nʼkawiri, koma ka 70 kuchulukitsa ndi kasanu nʼkawiri.
Ngati inu mukhululukira anthu pamene akuchimwirani, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani.
Komabe mwachifundo chanu chachikulu simuwatheretu kapena kuwataya pakuti ndinu Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo.
Zinthu zabwino zidzabwera kwa iye amene amapereka mowolowamanja ndi wokongoletsa mwaufulu,
amene amachita ntchito yake mwachilungamo.
Kukoma mtima kwa Ambuye Mulungu wathu kukhale pa ife;
tikhazikitsireni ntchito ya manja athu;
inde, khazikitsani ntchito ya manja athu.
Acessar a misericórdia
Cheguemos com confiança ao trono da graça. Ali encontramos misericórdia e graça para socorro no tempo oportuno.
Tiyeni tsono tiyandikire ku mpando waufumu, wachisomo mopanda mantha, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo chotithandiza pa nthawi yeniyeni.
Nʼchifukwa chake ine ndikukupemphani abale, mwa chifundo cha Mulungu, kuti mupereke matupi anu monga nsembe yamoyo, yopatulika ndi yokondweretsa Mulungu. Nsembeyi ndiye kupembedza kwanu kwa uzimu.
"Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha.
Pakuti inu mwapatsidwa mwayi osati ongokhulupirira Khristu kokha, koma wakumva zowawa mʼmalo mwa Khristu.
Hezekiya anatumiza uthenga mʼdziko lonse la Israeli ndi ku Yuda ndiponso analemba makalata ku Efereimu ndi Manase, oyitana anthu kuti abwere ku Nyumba ya Yehova ku Yerusalemu kudzakondwerera Paska wa Yehova, Mulungu wa Israeli. Mfumu ndi akuluakulu ake pamodzi ndi anthu onse a mu Yerusalemu anagwirizana kuti akondwerere Paska pa mwezi wachiwiri. Iwo sanathe kukondwerera pa nthawi yake chifukwa si ansembe ambiri amene anadziyeretsa ndiponso anthu anali asanasonkhane mu Yerusalemu. Chikonzerochi chinaoneka kuti chinali chabwino kwa mfumu pamodzi ndi anthu onse. Iwo anagwirizana zoti alengeze mu Israeli monse kuyambira ku Beeriseba mpaka ku Dani, kuyitana anthu kuti abwere ku Yerusalemu ndi kudzakondwerera Paska wa Yehova, Mulungu wa Israeli. Si ambiri amene ankachita chikondwererochi monga momwe kunalembedwera.
Molamulidwa ndi mfumu, amithenga anapita mu Israeli yense ndi Yuda ndi makalata ochokera kwa mfumu ndi kwa akuluakulu ake, olembedwa kuti,
"Aisraeli bwererani kwa Yehova, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Israeli, kuti abwerere kwa inu amene mwatsala, amene mwapulumuka mʼdzanja la mafumu a ku Asiriya. Musakhale ngati makolo anu ndi abale anu, amene anali osakhulupirika kwa Yehova Mulungu wa makolo awo kotero kuti anawachititsa kuti akhale chinthu chochititsa mantha, monga mukuoneramu. Musawumitse khosi monga anachitira makolo anu, Gonjerani Yehova. Bwerani ku malo opatulika, amene anawapatula kwamuyaya. Tumikirani Yehova Mulungu wanu kuti mkwiyo wake ukuchokereni. Ngati inu mubwerera kwa Yehova, pamenepo abale anu ndi ana anu adzachitiridwa chifundo ndi amene anawagwira ukapolo ndipo adzabwereranso ku dziko lino pakuti Yehova, Mulungu wanu ndi wokoma mtima ndi wachifundo. Iye sadzakufulatirani ngati inuyo mubwerera kwa Iye."
Amithenga aja anapita mzinda ndi mzinda wa ku Efereimu ndi Manase mpaka ku Zebuloni, koma anthu anawanyoza ndi kuwachita chipongwe. Komabe anthu ena a ku Aseri, Manase ndi Zebuloni anadzichepetsa ndipo anapita ku Yerusalemu. Dzanja la Mulungu linalinso pa anthu a ku Yuda, kuwapatsa mtima umodzi wochita zimene mfumu ndi akuluakulu ake analamula potsata mawu a Yehova.
Gulu lalikulu la anthu linasonkhana mu Yerusalemu kudzachita chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti pa mwezi wachiwiri. Anachotsa mu Yerusalemu maguwa ofukizira lubani ndipo anakawaponya mʼchigwa cha Kidroni.
Iwo anapha mwana wankhosa wa Paska pa tsiku la 14 la mwezi wachiwiri. Ansembe ndi Alevi anachita manyazi ndipo anadziyeretsa ndi kubweretsa nsembe zopsereza ku Nyumba ya Yehova. Ndipo anakhala mʼmalo awo a nthawi zonse potsatira zolembedwa mʼmalamulo a Mose munthu wa Mulungu. Ansembe anawaza magazi amene anawapatsa Alevi. Popeza ambiri mʼgululo anali asanadziyeretse, Alevi anapha ana ankhosa a Paska a iwo amene, mwa mwambo, anali osayeretsedwa ndipo sakanatha kupereka ana ankhosa awo kwa Yehova. Ngakhale kuti ambiri mwa anthu ochokera ku Efereimu, Manase, Isakara ndi Zebuloni sanadziyeretse okha, komabe anadya Paska motsutsana ndi zimene zinalembedwa. Koma Hezekiya anawapempherera, kunena kuti, "Yehova wabwino, khululukirani aliyense amene wayika mtima wake kufunafuna Yehova, Mulungu wa makolo ake, ngakhale ali wosayeretsedwa molingana ndi malamulo a malo opatulika." Ndipo Yehova anamvera Hezekiya ndipo anachiritsa anthuwo.
Aisraeli amene anali mu Yerusalemu anachita chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti kwa masiku asanu ndi awiri akusangalala kwambiri, pamene Alevi ndi ansembe amayimbira Yehova tsiku lililonse, akuyimbira zida zamatamando za Yehova.
Hezekiya anayankhula molimbikitsa Alevi onse amene anaonetsa kumvetsa bwino za kutumikira Yehova. Kwa masiku asanu ndi awiri anadya gawo lawo ndi kupereka nsembe zachiyanjano ndi kutamanda Yehova, Mulungu wa makolo awo.
Ndipo msonkhano wonse unagwirizana zopitiriza chikondwerero kwa masiku ena asanu ndi awiri. Kotero kwa masiku ena asanu ndi awiri anachita chikondwererocho mosangalala. Hezekiya mfumu ya Yuda anapereka ngʼombe zamphongo 1,000 ndi nkhosa ndi mbuzi 7,000 ku msonkhanoko ndipo akuluakulu ake anapereka ngʼombe zamphongo 1,000, nkhosa ndi mbuzi 10,000. Ansembe ambiri anadziyeretsa. Gulu lonse la ku Yuda linasangalala, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi ndi onse amene anasonkhana ochokera ku Israeli, kuphatikizanso alendo amene anachokera ku Israeli ndi amene amakhala ku Yuda. Munali chikondwerero chachikulu mu Yerusalemu, pakuti kuyambira masiku a Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israeli sizinachitikepo zotere mu Yerusalemu. Ansembe ndi Alevi anayimirira kudalitsa anthu, ndipo Mulungu anawamvera pakuti pemphero lawo linafika kumwamba, malo ake oyera.
"Ngati munthu asudzula mkazi wake
ndipo mkaziyo nʼkuchoka nakakwatiwa ndi mwamuna wina,
kodi mwamuna woyambayo angathe kumutenganso mkaziyo?
Kodi atatero sindiye kuti dzikolo layipitsidwa kwambiri?
Koma iwe Israeli wachita zadama ndi zibwenzi zambiri.
Komabe bwerera kwa ine,"
akutero Yehova.
"Tayangʼana ku zitunda zowuma.
Kodi aliponso malo ena amene iwe sunachitepo zadama?
Iwe unkakhala mʼmbali mwa njira kumadikira zibwenzi zako,
ngati Mluya wobisalira anthu mʼchipululu.
Inu mwayipitsa dziko ndi zadama zanu
ndi ntchito zanu zoyipa.
Nʼchifukwa chake Yehova wayimitsa mvula,
ndipo mvula ya nthawi ya masika sinagwe.
Komabe uli ndi maonekedwe a mkazi wachiwerewere;
ndipo sukuchita manyazi ndi pangʼono pomwe.
Kodi iwe siposachedwa pomwepa pamene wanena
kuti, ‘Abambo anga, Inu bwenzi langa la unyamata wanga,
kodi mudzandikwiyira nthawi zonse?
Kodi ukali wanu udzakhalabe mpaka muyaya?’
Umu ndimo mmene umayankhulira,
koma umapitirizabe kuchita zoyipa monga momwe umathera."
Pa nthawi ya Mfumu Yosiya Yehova anandiwuza kuti, "Kodi waona zomwe Israeli wosakhulupirika uja wachita? Anakwera pa phiri lililonse lalitali ndi kupita pa tsinde pa mtengo uliwonse wogudira kukapembedza. Choncho anachita za chiwerewere kumeneko. Ndinaganiza kuti atachita zonsezi, adzabwerera kwa Ine, koma sanabwerere, ndipo mlongo wake wosakhulupirika uja, Yuda, anaziona zimenezi. Anaona kuti ndinasudzula Israeli wosakhulupirikayo ndi kumupirikitsa chifukwa cha zigololo zake. Komabe Yuda mʼbale wake wosakhulupirika uja sanaope, nayenso anapita kukachita chigololo. Chiwerewere cha Israeli chinali chochititsa manyazi kotero kuti chinayipitsa dziko lonse. Anachita chigololo popembedza mafano a miyala ndi mitengo. Israeli atachita zonsezi, Yuda mʼbale wake wosakhulupirika uja sanabwerere kwa Ine ndi mtima wake wonse, koma mwachiphamaso chabe," akutero Yehova.
Yehova anandiwuza kuti, "Kusakhulupirika kwa Israeli nʼkochepa kuyerekeza ndi kusakhulupirika kwa Yuda. Pita ukalalikire kumpoto uthenga wakuti,
" ‘Israeli wosakhulupirikawe, bwerera,’ akutero Yehova.
‘Sindidzakukalipira mpaka kalekale,
pakuti ndine wachifundo,’ akutero Yehova.
‘Sindidzakukwiyira mpaka kalekale.
Ungovomera kulakwa kwako
kuti unawukira Yehova Mulungu wako.
Vomera kuti unayendayenda kukapembedza milungu yachilendo
pansi pa mtengo uliwonse wogudira,
ndiponso kuti sunandimvere,’ "
akutero Yehova.
"Bwererani, ana osakhulupirika, pakuti ndine mbuye wanu," akutero Yehova. "Ndinakusankhani, mmodzimmodzi kuchokera ku mudzi uliwonse ndiponso awiriawiri kuchokera ku banja lililonse. Ndipo ndidzakupatsani abusa a pamtima panga amene adzakutsogolerani mwanzeru ndi mwaluntha. Masiku amenewo mukadzachulukana kwambiri mʼdzikomo, anthu sadzanenanso za ‘Bokosi la Chipangano la Yehova’ kapena kuliganizira. Sadzalikumbukiranso kapena kulifuna, ndipo sadzapanganso lina,"
akutero Yehova.
Nthawi imeneyo adzatcha Yerusalemu Mpando Waufumu wa Yehova, ndipo mitundu yonse ya anthu idzasonkhana mu Yerusalemu pamaso pa Yehova. Sadzawumiriranso kutsata mitima yawo yoyipa. Masiku amenewo fuko la Yuda lidzaphatikizana ndi fuko la Israeli, onse pamodzi adzachokera ku dziko la kumpoto kupita ku dziko limene ndinapatsa makolo awo, kuti likhale cholowa.
"Ine mwini ndinati,
" ‘Ndikanakonda bwanji kukukhazikani pakati pa ana anga
ndikukupatsani dziko labwino kwambiri,
cholowa chokongola kwambiri kuposa cha mitundu ina ya anthu.’
Ndinaganiza kuti mudzanditcha Ine ‘Atate’
ndi kuti simudzaleka kunditsata.
Koma monga mkazi wosakhulupirika amasiya mwamuna wake,
momwemonso inu mwakhala osakhulupirika kwa Ine, inu fuko la Israeli,"
akutero Yehova.
Mawu akumveka pa magomo,
Aisraeli akulira ndi kupempha chifundo
chifukwa anatsata njira zoyipa
ndi kuyiwala Yehova Mulungu wawo.
Inu mukuti, "Bwererani, anthu osakhulupirika;
ndidzachiritsa kubwerera mʼmbuyo kwanu."
"Inde, tidzabwerera kwa Inu
pakuti ndinu Yehova Mulungu wathu.
Ndithu kupembedza pa magomo
komanso kuchita maphwando pa mapiri zilibe phindu.
Zoonadi chipulumutso cha Israeli
chili mwa Yehova Mulungu wathu basi.
Kuyambira pa ubwana wathu milungu yochititsa manyazi ija yakhala ikutiwonongetsa phindu
la ntchito za makolo athu,
nkhosa ndi ngʼombe zawo,
ana awo aamuna ndi aakazi.
Tilekeni tigone pansi mwa manyazi,
ndipo kunyozeka kwathu kutiphimbe.
Paja tachimwira Yehova Mulungu wathu,
ife pamodzi ndi makolo athu
kuyambira nthawi ya ubwana wathu mpaka lero lino
sitinamvere Yehova Mulungu wathu."